Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 12:40 - Buku Lopatulika

40 pakuti monga Yona anali m'mimba mwa chinsomba masiku atatu ndi usiku wake, chomwecho Mwana wa Munthu adzakhala mumtima mwa dziko lapansi masiku atatu ndi usiku wake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

40 pakuti monga Yona anali m'mimba mwa chinsomba masiku atatu ndi usiku wake, chomwecho Mwana wa Munthu adzakhala mumtima mwa dziko lapansi masiku atatu ndi usiku wake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

40 Monga Yona uja anali m'mimba mwa chinsomba chija masiku atatu, usana ndi usiku, chomwechonso Mwana wa Munthu adzakhala m'kati mwa nthaka masiku atatu, usana ndi usiku.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

40 Pakuti monga Yona anali mʼmimba mwa nsomba yayikulu masiku atatu, usana ndi usiku, momwemonso Mwana wa Munthu adzakhala masiku atatu, usana ndi usiku, mʼkati mwa nthaka.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 12:40
12 Mawu Ofanana  

Anabweza malire a Israele kuyambira polowera ku Hamati mpaka ku Nyanja ya Araba, monga mwa mau a Yehova Mulungu wa Israele, amene ananena ndi dzanja la mtumiki wake Yona mwana wa Amitai mneneriyo, ndiye wa Gatihefere.


Koma iwo amene afuna moyo wanga kuti auononge, adzalowa m'munsi mwake mwa dziko.


Koma Yehova anaikiratu chinsomba chachikulu chimeze Yona; ndipo Yona anali m'mimba mwa nsombayi masiku atatu usana ndi usiku.


pakuti Mwana wa Munthu ali mwini tsiku la Sabata.


Kuyambira pamenepo Yesu anayamba kuwalangiza ophunzira ake, kuti kuyenera Iye amuke ku Yerusalemu, kukazunzidwa zambiri ndi akulu, ndi ansembe aakulu, ndi alembi; ndi kukaphedwa, ndi tsiku lachitatu kuuka kwa akufa.


ndipo adzamupha Iye, ndipo Iye adzauka tsiku lachitatu. Ndipo iwo anali ndi chisoni chachikulu.


nati, Nanga Iwe, wopasula Kachisi, ndi kummanganso masiku atatu, tadzipulumutsa wekha; ngati uli Mwana wa Mulungu, tatsika pamtandapo.


Iye mulibe muno iai; pakuti anauka, monga ananena. Idzani muno mudzaone malo m'mene anagonamo Ambuye.


Ndipo Yesu ananena kwa iye, Ankhandwe ali nazo nkhwimba zao, ndi mbalame za m'mlengalenga zisa zao, koma Mwana wa Munthu alibe potsamira mutu wake.


Yesu anayankha nati kwa iwo, Pasulani Kachisi uyu, ndipo masiku atatu ndidzamuutsa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa