Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 24:20 - Buku Lopatulika

20 Ndipo Arauna anayang'ana naona mfumuyo ndi anyamata ake alikubwera kwa iye; natuluka Arauna naweramira pamaso pa mfumu nkhope yake pansi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Ndipo Arauna anayang'ana naona mfumuyo ndi anyamata ake alikubwera kwa iye; natuluka Arauna naweramira pamaso pa mfumu nkhope yake pansi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Ndipo Arauna atapenya chakunsi, adaona mfumu ikudza kwa iye pamodzi ndi atumiki ake. Pomwepo Araunayo adapita kukalambira mfumu choŵerama pansi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Arauna atayangʼana ndi kuona mfumu ndi anthu ake akubwera kumene kunali iye, iyeyo anatuluka ndi kuwerama pamaso pa mfumu mpaka nkhope yake kugunda pansi.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 24:20
7 Mawu Ofanana  

Ndipo anatukula maso ake, nayang'ana, taonani, anthu atatu anaima pandunji pake; pamene anaona iwo, anawathamangira kuchoka ku khomo la hema kukakomana nao, nawerama pansi, nati,


pa tsiku lachitatu, onani, munthu anatuluka ku zithando za Saulo, ali ndi zovala zake zong'ambika, ndi dothi pamutu pake; ndipo kunatero kuti iye, pofika kwa Davide, anagwa pansi namgwadira.


Ndipo Davide anakwerako monga mwa kunena kwa Gadi, monga adalamulira Yehova.


Arauna nati, Mbuye wanga mfumu, mwadzeranji kwa mnyamata wanu? Ndipo Davide, anati, Kugula dwale lako ili, kuti ndimangirepo Yehova guwa la nsembe, kuti mliriwo ulekeke kwa anthu.


Ndipo iye anamlambira, nati, Mnyamata wanu ndani, kuti mulikupenya galu wakufa monga ine.


Potero anagwa nkhope yake pansi, nadziweramira pansi, nanena naye, Mwandikomera mtima chifukwa ninji kuti mundisamalira ine, popeza ndine mlendo?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa