Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 25:23 - Buku Lopatulika

23 Ndipo Abigaile pakuona Davide, anafulumira kutsika pabulu, nagwa pamaso pa Davide nkhope yake pansi, namgwadira,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Ndipo Abigaile pakuona Davide, anafulumira kutsika pa bulu, nagwa pamaso pa Davide nkhope yake pansi, namgwadira,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Abigaile ataona Davide, adatsika pa bulu msangamsanga, nadzigwetsa chafufumimba pamaso pake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Abigayeli ataona Davide, anatsika pa bulu wake mofulumira ndipo anadzigwetsa pansi pamaso pa Davide.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 25:23
12 Mawu Ofanana  

pa tsiku lachitatu, onani, munthu anatuluka ku zithando za Saulo, ali ndi zovala zake zong'ambika, ndi dothi pamutu pake; ndipo kunatero kuti iye, pofika kwa Davide, anagwa pansi namgwadira.


Ndipo pamene mkazi wa ku Tekowayo anati alankhule ndi mfumuyo, anagwa nkhope yake pansi, namlambira, nati, Ndithandizeni mfumu.


Ndipo Ahimaazi anafuula, nanena ndi mfumu, Mtendere. Ndipo anawerama pamaso pa mfumu ndi nkhope yake pansi, nati, Alemekezeke Yehova Mulungu wanu amene anapereka anthu akukwezera dzanja lao pa mbuye wanga mfumu.


Ndipo Mefiboseti mwana wa Yonatani, mwana wa Saulo, anafika kwa Davide, nagwa nkhope yake pansi, namlambira. Ndipo Davide anati, Mefiboseti! Nayankha iye, Ndine mnyamata wanu.


Ndipo pofika Davide kwa Orinani, Orinaniyo anapenyetsa, naona Davide, natuluka kudwale, nawerama kwa Davide, nkhope yake pansi.


Ndipo kunali, m'mene anamdzera, anamkangamiza mwamuna wake kuti apemphe atate wake ampatse munda; ndipo anatsika pabulu; pamenepo Kalebe ananena naye, Ufunanji?


Ndipo kunali, m'mene anamdzera, anamkakamiza mwamuna wake kuti apemphe atate wake ampatse munda; natsika pabulu wake; ndipo Kalebe ananena naye, Ufunanji?


Potero anagwa nkhope yake pansi, nadziweramira pansi, nanena naye, Mwandikomera mtima chifukwa ninji kuti mundisamalira ine, popeza ndine mlendo?


Pomwepo pochoka mnyamatayo, Davide, anauka chakumwera, nagwa nkhope yake pansi, nawerama katatu; ndipo iwowa anapsompsonana, nalirirana, kufikira Davide analiritsa.


Bwino lake Davide yemwe ananyamuka, natuluka m'phangamo, nafuulira Saulo, nati, Mbuye wanga, mfumu. Ndipo pakucheuka Saulo, Davide anaweramira nkhope yake pansi, namgwadira.


Ndipo atagwadira pa mapazi ake anati, Pa ine, mbuye wanga, pa ine pakhale uchimowo; ndipo mulole mdzakazi wanu alankhule m'makutu anu, nimumvere mau a mdzakazi wanu.


Ndipo iye ananyamuka, nawerama nkhope yake pansi, nati, Onani, mdzakazi wanu ali kapolo wakusambitsa mapazi a anyamata a mbuye wanga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa