Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 25:22 - Buku Lopatulika

22 Mulungu alange adani a Davide, ndi kuonjezerapo, ngati ndisiyapo kufikira kuunika kwa m'mawa, kanthu konse ka iye, kangakhale kamwana kamphongo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Mulungu alange adani a Davide, ndi kuonjezerapo, ngati ndisiyapo kufikira kuunika kwa m'mawa, kanthu konse ka iye, kangakhale kamwana kamphongo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Mulungu andilange ndithu ngati m'maŵa ndikhale nditasiyapo ngakhale munthu wamwamuna mmodzi mwa anthu onse amene ali nawo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Mulungu andilange kwambiri ngati pofika mmawa nditakhale nditasiyako ngakhale munthu mmodzi mwa onse amene ali nawo.”

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 25:22
9 Mawu Ofanana  

chifukwa chake, taona ndidzafikitsa choipa pa nyumba ya Yerobowamu, ndi kugulula mwana wamwamuna yense wa Yerobowamu womangika ndi womasuka mu Israele, ndipo ndidzachotsa psiti nyumba yonse ya Yerobowamu, monga munthu achotsa ndowe kufikira idatha yonse.


Ndipo kunali, atalowa ufumu wake, nakhala pa mpando wachifumu wake, anawakantha onse a m'nyumba ya Baasa, osamsiyira mwana wamwamuna ndi mmodzi yense, kapena wa abale ake, kapena wa mabwenzi ake.


Taona, ndidzakufikitsira choipa, ndi kuchotsa mbumba yako psiti; ndipo ndidzalikhira Ahabu mwana wamwamuna yense, ndi yense womangika ndi womasuka mu Israele;


Popeza nyumba yonse ya Ahabu idzaonongeka, ndipo ndidzalikhira Ahabu ana aamuna onse womangika ndi womasuka mu Israele.


kumene mudzafera inu ine ndidzafera komweko, ndi kuikidwa komweko; andilange Yehova naonjezeko, chilichonse chikasiyanitsa inu ndi ine, koma imfa ndiyo.


Pamenepo Saulo anati, Mulungu andilange, naonjezereko, pakuti udzafa ndithu, Yonatani.


Mulungu alange Yonatani, ndi kuonjezapo, ngati atate wanga akondwera kukuchitira choipa, ine osakuululira, ndi kukuchotsa kuti upite mumtendere; ndipo Yehova akhale nawe, monga anakhala naye atate wanga.


Chomwecho Yonatani anapangana pangano ndi nyumba ya Davide, ndipo Yehova anakwaniritsa izi polanga adani a Davide.


Ndipo anati, Anakuuza chinthu chanji? Usandibisire ine. Mulungu akulange, ndi kuonjezapo, ngati undibisira chimodzi cha zonse zija adanena nawe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa