Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 25:21 - Buku Lopatulika

21 Koma Davide adanena, Zoonadi ndasunga chabe zake zonse za kaja kanali nazo m'chipululu, sikadasowe kanthu ka zake zonse; ndipo iye anandibwezera zoipa m'malo mwa zabwino.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Koma Davide adanena, Zoonadi ndasunga chabe zake zonse za kaja kanali nazo m'chipululu, sikadasowa kanthu ka zake zonse; ndipo iye anandibwezera zoipa m'malo mwa zabwino.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Nthaŵiyo nkuti Davide atanena kuti, “Ndithudi ndidavutika pachabe kutchinjiriza zinthu zonse za munthu ameneyu, zimene anali nazo ku chipululu, kotero kuti palibe kanthu nkamodzi komwe pa zinthu zakezo kamene kadasoŵa. Koma iye wandibwezera zoipa m'malo mwa zabwino.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Nthawiyi nʼkuti Davide atanena kuti, “Kani ndinalondera pachabe katundu wa munthu uyu mʼchipululu muja! Ndipotu palibe kanthu nʼkamodzi komwe kake kamene kanasowa. Tsono wandibwezera zoyipa mʼmalo mwa zabwino.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 25:21
19 Mawu Ofanana  

Atatuluka m'mzinda asanamuke patali, Yosefe anati kwa tsanyumba wake, Tanyamuka, talondola anthu aja, ukawapeza unene nao, Chifukwa chanji mwabwezera zoipa m'malo mwa zabwino?


Ndiwo ana a opusa, inde ana a anthu opanda dzina; anawaingitsa kuwachotsa m'dziko.


Andibwezera choipa m'malo mwa chokoma, inde, asaukitsa moyo wanga.


Leka kupsa mtima, nutaye mkwiyo; usavutike mtima ungachite choipa.


Ndipo iwo akubwezera choipa pa chabwino atsutsana nane, popeza nditsata chabwino.


Wobwezera zabwino zoipa, zoipa sizidzamchokera kwao.


Kodi choipa chibwezedwe pa chabwino? Pakuti akumbira moyo wanga dzenje. Mukumbukire kuti ndinaima pamaso panu kuwanenera zabwino, kuwachotsera iwo ukali wanu.


Musagonje kwa choipa, koma ndi chabwino gonjetsani choipa.


Kwiyani, koma musachimwe; dzuwa lisalowe muli chikwiyire,


Chiwawo chonse, ndi kupsa mtima, ndi mkwiyo, ndi chiwawa, ndi mwano zichotsedwe kwa inu, ndiponso choipa chonse.


Penyani kuti wina asabwezere choipa womchitira choipa; komatu nthawi zonse mutsatire chokoma, kwa anzanu, ndi kwa onse.


Pakuti, kumva zowawa chifukwa cha kuchita zabwino, ndi kumva zowawa chifukwa cha kuchita zoipa, nkwabwino kumva zowawa chifukwa cha kuchita zabwino, ngati chitero chifuniro cha Mulungu.


osabwezera choipa ndi choipa, kapena chipongwe ndi chipongwe, koma penatu madalitso; pakuti kudzatsata ichi mwaitanidwa, kuti mukalandire dalitso.


Ndipo Davide anati kwa anthu ake, Munthu yense wa inu amangirire lupanga lake. Namangirira munthu yense lupanga lake; ndi Davide yemwe anamangirira lupanga lake; ndipo anakwera kumtsata Davide monga anthu mazana anai, koma mazana awiri anadika akatundu.


Koma anthu aja anatichitira zabwino ndithu, sanatichititse manyazi, ndi panalibe kanthu kadatisowa, nthawi zonse tinali kuyenderana nao kubusa kuja;


Ndipo kudatero pakuberekeka iye pabulu wake, natsikira pamalo obisika a m'phirilo, onani, Davide ndi anthu ake analikutsikira kwa iye; iye nakomana nao.


Ndipo tsono ndamva kuti muli nao osenga nkhosa; abusa anu amene anali ndi ife, sitinawachititse manyazi, ndipo panalibe kanthu kao kadasowa, nthawi yonse anakhala iwo ku Karimele.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa