Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 4:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo munthu wa fuko la Benjamini anathamanga kuchokera ku khamu la ankhondo, nafika ku Silo tsiku lomwelo, ndi zovala zake zong'ambika, ndi dothi pamutu pake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo munthu wa fuko la Benjamini anathamanga kuchokera ku khamu la ankhondo, nafika ku Silo tsiku lomwelo, ndi zovala zake zong'ambika, ndi dothi pamutu pake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Munthu wina wa fuko la Benjamini adathaŵa kunkhondoko nakafika ku Silo tsiku lomwelo. Anali atang'amba zovala zake ndi kudzithira dothi kumutu, kuwonetsa chisoni.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Tsiku lomwelo munthu wina wa fuko la Benjamini anathawa ku nkhondo ndipo anafika ku Silo. Iyeyu zovala zake zinali zongʼamba ndipo anadzithira dothi kumutu kuonetsa chisoni.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 4:12
9 Mawu Ofanana  

pa tsiku lachitatu, onani, munthu anatuluka ku zithando za Saulo, ali ndi zovala zake zong'ambika, ndi dothi pamutu pake; ndipo kunatero kuti iye, pofika kwa Davide, anagwa pansi namgwadira.


Ndipo Tamara anathira phulusa pamutu pake, nang'amba chovala cha mawangamawanga chimene analikuvala, nagwira dzanja lake pamutu pake, namuka nayenda, nalira komveka.


Ndipo kunali pakufika Davide ku mutu wa phiri, kumene amapembedza Mulungu, onani, Husai Mwariki anadzakomana naye ali ndi malaya ake ong'ambika, ndi dothi pamutu pake.


Ndipo tsiku la makumi awiri mphambu anai la mwezi uno ana a Israele anasonkhana ndi kusala, ndi kuvala chiguduli, ndipo anali ndi fumbi.


Ndipo pokweza maso ao ali kutali, sanamdziwe, nakweza mau ao, nalira; nang'amba yense malaya ake, nawaza fumbi kumwamba ligwe pamitu pao.


pamenepo ndidzayesa nyumba iyi ifanane ndi Silo, ndipo ndidzayesa mzinda uwu chitemberero cha kwa mitundu yonse ya dziko lapansi.


kuti tsiku lomwelo wopulumukayo adzakudzera, kukumvetsa m'makutu mwako?


nadzamveketsa mau ao pa iwe, nadzalira mowawa mtima, nadzathira fumbi pamitu pao, nadzakunkhulira m'maphulusa,


Ndipo Yoswa anang'amba zovala zake, nagwa nkhope yake pansi, ku likasa la Yehova, mpaka madzulo, iye ndi akuluakulu a Israele, nathira fumbi pamitu pao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa