1 Samueli 4:13 - Buku Lopatulika13 Pakufika iye, onani, Eli analikukhala pampando m'mbali mwa njira, alikuyang'anira, popeza mtima wake unanthunthumira chifukwa cha likasa la Mulungu. Pamene munthu uja anafika m'mzindamo, nanena izi, a m'mzinda monse analira. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201413 Pakufika iye, onani, Eli analikukhala pampando m'mbali mwa njira, alikuyang'anira, popeza mtima wake unanthunthumira chifukwa cha likasa la Mulungu. Pamene munthu uja anafika m'mudzimo, nanena izi, a m'mudzi monse analira. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa13 Atafika, adapeza Eli atakhala pa mpando pambali pa mseu akungoyang'ana, poti ankadera nkhaŵa Bokosi lachipangano la Chauta lija. Pamene Mbenjamini uja adaloŵa mumzindamo, nayamba kusimba zimene zidaachitika kunkhondoko, anthu onse amumzinda adalira kwambiri. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero13 Atafika, anapeza Eli atakhala pa mpando wake mʼmbali mwa msewu, akungoyangʼana, pakuti ankadera nkhawa Bokosi la Mulungu. Munthuyo atalowa mu mzindamo ndi kufotokoza zimene zinachitika ku nkhondo, anthu onse a mu mzindamo anayamba kulira. Onani mutuwo |