Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 4:14 - Buku Lopatulika

14 Ndipo Eli, pakumva kubuma kwa kulira kwao, anati, Alikupokoseranji? Ndipo munthuyo anafulumira, nadza nauza Eli.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndipo Eli, pakumva kubuma kwa kulira kwao, anati, Alikupokoseranji? Ndipo munthuyo anafulumira, nadza nauza Eli.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Eli atamva kulirako, adafunsa kuti, “Kodi kulira kumeneku ndiye kuti kwachitika chiyani?” Tsono munthu uja adapita msanga kwa Eli, nayamba kumufotokozera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Eli atamva kulirako anafunsa kuti, “Kodi phokosoli likutanthauza chiyani?” Tsono munthu wa fuko la Benjamini uja anapita msanga kwa Eli kukamufotokozera.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 4:14
3 Mawu Ofanana  

Iwe wokhala mu Aroere, ima panjira, nusuzumire umfunse iye amene athawa, ndi mkazi amene apulumuka; nuti, Chachitidwa chiyani?


Pakufika iye, onani, Eli analikukhala pampando m'mbali mwa njira, alikuyang'anira, popeza mtima wake unanthunthumira chifukwa cha likasa la Mulungu. Pamene munthu uja anafika m'mzindamo, nanena izi, a m'mzinda monse analira.


Koma Eli anali ndi zaka makumi asanu ndi anai kudza zisanu ndi zitatu; ndipo maso ake anangokhala tong'o osapenya.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa