Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 4:15 - Buku Lopatulika

15 Koma Eli anali ndi zaka makumi asanu ndi anai kudza zisanu ndi zitatu; ndipo maso ake anangokhala tong'o osapenya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Koma Eli anali ndi zaka makumi asanu ndi anai kudza zisanu ndi zitatu; ndipo maso ake anangokhala tong'o osapenya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Nthaŵiyo nkuti Eli ali nkhalamba ya zaka 98, maso ake atachita khungu, kotero kuti sankathanso kupenya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Nthawiyo nʼkuti Eli ali wa zaka 98 ndipo maso ake anali atachita khungu kotero kuti samatha kuona.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 4:15
5 Mawu Ofanana  

Ndipo panali atakalamba Isaki, ndi maso ake anali akhungu losaona nalo, anamuitana Esau mwana wake wamwamuna wamkulu, nati kwa iye, Mwana wanga; ndipo anati kwa iye, Ndine pano.


Natero mkazi wa Yerobowamu, nanyamuka nanka ku Silo, nalowa m'nyumba ya Ahiya. Koma Ahiya sanathe kupenya, popeza maso ake anali tong'o, chifukwa cha ukalamba wake.


Masiku a zaka zathu ndiwo zaka makumi asanu ndi awiri, kapena tikakhala nayo mphamvudi zaka makumi asanu ndi atatu; koma teronso kukula kwao kumati chivuto ndi chopanda pake; pakuti kumapitako msanga ndipo tithawa ife tomwe.


Ndipo kunali nthawi yomweyo Eli atagona m'malo mwake (maso ake anayamba chizirezire osatha kupenya bwino);


Ndipo Eli, pakumva kubuma kwa kulira kwao, anati, Alikupokoseranji? Ndipo munthuyo anafulumira, nadza nauza Eli.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa