Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 37:34 - Buku Lopatulika

34 Yakobo ndipo anang'amba malaya ake, na vala chiguduli m'chuuno mwake namlirira mwana wake masiku ambiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

34 Yakobo ndipo anang'amba malaya ake, navala chiguduli m'chuuno mwake namlirira mwana wake masiku ambiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

34 Yakobe adang'amba zovala zake, navala chiguduli m'chiwuno, chifukwa cha chisoni. Adalira maliro a mwana wakeyo nthaŵi yaitali.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

34 Pamenepo Yakobo anangʼamba zovala zake, navala chisaka mʼchiwuno mwake. Iye analira maliro a mwana wake masiku ambiri.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 37:34
32 Mawu Ofanana  

Ndipo Rubeni anabwera kudzenje, ndipo taonani, Yosefe mulibe m'dzenjemo: ndipo iye anang'amba nsalu yake.


Ndipo iye anati, Mwana wanga sadzatsikira ndi inu, chifukwa kuti mkulu wake wafa, ndipo watsala iye yekha; ngati choipa chikamgwera iye m'njira m'mene mupitamo, inu mudzatsitsira ndi chisoni imvi zanga kumanda.


ndipo anang'amba zovala zao, nasenzetsa yense bulu wake, nabwera kumzinda.


Pomwepo Davide anagwira zovala zake nazing'amba; nateronso anthu onse okhala naye.


Ndipo Davide anati kwa Yowabu ndi kwa anthu onse okhala naye, Ng'ambani zovala zanu, ndi kudzimangira ziguduli m'chuuno, nimulire Abinere. Ndipo mfumu Davide anatsata chithatha.


Pamenepo anyamata ake anati kwa iye, Taonani, tidamva ife kuti mafumu a nyumba ya Israele ndi mafumu achifundo; tiyeni tivale chiguduli m'chuuno mwathu, ndi zingwe pamitu pathu, titulukire kwa mfumu ya Israele, kapena adzakusungirani moyo.


Ndipo kunali, pakumva Ahabu mau amenewa, anang'amba zovala zake, navala chiguduli pathupi pake, nasala kudya, nagona pachiguduli, nayenda nyang'anyang'a.


Ndipo kunali, atamva mfumu Hezekiya, anang'amba zovala zake, nafundira chiguduli, nalowa m'nyumba ya Yehova.


Ndipo Elisa anapenya, nafuula, Atate wanga, atate wanga, galeta wa Israele ndi apakavalo ake! Koma analibe kumpenyanso; nagwira zovala zakezake, nazing'amba pakati.


Ndipo kunali, atamva mfumu mau a m'buku la chilamulo, inang'amba zovala zake.


Ndipo Davide anakweza maso ake, naona mthenga wa Yehova alikuima pakati padziko ndi thambo, ali nalo lupanga losolola m'dzanja lake, lotambasukira pa Yerusalemu. Pamenepo Davide ndi akulu ovala ziguduli anagwa nkhope zao pansi.


Ndipo Efuremu atate wao, anachita maliro masiku ambiri, ndi abale ake anadza kudzamtonthoza mtima.


Ndipo tsiku la makumi awiri mphambu anai la mwezi uno ana a Israele anasonkhana ndi kusala, ndi kuvala chiguduli, ndipo anali ndi fumbi.


Pamenepo Yobu ananyamuka, nang'amba malaya ake, nameta mutu wake, nagwa pansi, nalambira,


Ndadzisokerera chiguduli kukhungu langa. Ndipo ndaipsa mphamvu yanga m'fumbi.


Ndipo pokweza maso ao ali kutali, sanamdziwe, nakweza mau ao, nalira; nang'amba yense malaya ake, nawaza fumbi kumwamba ligwe pamitu pao.


Ndipo chovala changa ndinayesa chiguduli, koma amandiphera mwambi.


Nthunthumirani, inu akazi, amene mulinkukhala phee; vutidwani, inu osasamalira, vulani mukhale maliseche, nimumange chiguduli m'chuuno mwanu.


Ndipo anafika Eliyakimu, mwana wa Hilikiya, amene anali wapa nyumba, ndi Sebina, mlembi, ndi Yowa, mwana wa Asafu, mkumbutsi, kwa Hezekiya ndi zovala zao zong'ambika, namuuza iye mau a kazembeyo.


Ndipo sanaope, sanang'ambe nsalu zao, kapena mfumu, kapena atumiki ake aliyense amene anamva mau onsewa.


Pakuti mitu yonse ili yadazi, ndipo ndevu zili zometedwa; pa manja onse pali pochekedwachekedwa, ndi pachiuno chiguduli.


ndipo ng'ambani mitima yanu, si zovala zanu ai; ndi kutembenukira kwa Yehova Mulungu wanu; pakuti Iye ndiye wachisomo, ndi wodzala chifundo, wosapsa mtima msanga, ndi wochuluka kukoma mtima, ndi woleka choipacho.


Tsoka kwa iwe, Korazini! Tsoka kwa iwe, Betsaida! Chifukwa ngati zamphamvu zimene zachitidwa mwa inu zikadachitidwa mu Tiro ndi mu Sidoni, akadatembenuka mtima kalekale m'ziguduli ndi m'phulusa.


Pomwepo mkulu wa ansembe anang'amba zovala zake, nati, Achitira Mulungu mwano; tifuniranji mboni zina? Onani, tsopano mwamva mwanowo;


Pamene anamva atumwi Paulo ndi Barnabasi, anang'amba zofunda zao, natumphira m'khamu,


Ndipo Yoswa anang'amba zovala zake, nagwa nkhope yake pansi, ku likasa la Yehova, mpaka madzulo, iye ndi akuluakulu a Israele, nathira fumbi pamitu pao.


Ndipo ndidzalamulira mboni zanga ziwiri, ndipo zidzanenera masiku chikwi chimodzi ndi mazana awiri amphambu makumi asanu ndi limodzi, zovala chiguduli.


Ndipo kunali, pakumuona anang'amba zovala zake, nati, Tsoka ine, mwana wanga, wandiweramitsa kwakukulu, ndiwe wa iwo akundisaukitsa ine; pakuti ndamtsegulira Yehova pakamwa panga ine, ndipo sinditha kubwerera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa