Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 37:35 - Buku Lopatulika

35 Ndipo ana aamuna ake onse ndi ana aakazi onse anauka kuti amtonthoze: koma anakana kutonthozedwa; ndipo anati, Pakuti ndidzatsikira kumanda kwa mwana wanga, ndilinkulirabe. Atate wake ndipo anamlirira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

35 Ndipo ana amuna ake onse ndi ana akazi onse anauka kuti amtonthoze: koma anakana kutonthozedwa; ndipo anati, Pakuti ndidzatsikira kumanda kwa mwana wanga, ndilinkulirabe. Atate wake ndipo anamlirira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

35 Ana ake onse aamuna ndi aakazi, adabwera kuti amtonthoze koma iye adakana, adati, “Ndidzakhala ndikulira mwana wanga mpaka kumanda komwe kuli iyeko.” Choncho adapitirirabe kulira chifukwa cha Yosefe mwana wake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

35 Ngakhale kuti ana ake onse aamuna ndi aakazi anasonkhana kudzamutonthoza, iye anakana kutonthozedwa. Iye anati, “Ayi. Ndidzalira mpaka ndidzapite kwa mwana wanga ku manda.” Choncho Israeli anapitirirabe kulira mwana wake.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 37:35
18 Mawu Ofanana  

Ndipo Abrahamu anamwalira, nafa mu ukalamba wake wabwino, nkhalamba ya zaka zambiri; natengedwa akhale ndi a mtundu wake.


Ndipo Labani anayankha nati kwa Yakobo, Akaziwa ndiwo ana anga, anawa ndiwo ana anga, zowetazi ndizo zoweta zanga ndi zonse ulinkuziona ndizo zanga: nanga ndidzachitira ine chiyani lero kwa ana anga aakazi amenewa, kapena ana ao amene anabala?


Ndipo Isaki anatsirizika nafa, nasonkhanitsidwa kwa anthu a mtundu wake, wokalamba ndi wa masiku okwanira: ndipo Esau ndi Yakobo ana ake aamuna anamuika iye.


Koma ife tinati kwa iye, Tili anthu oona; sitili ozonda;


Ndipo iye anati, Mwana wanga sadzatsikira ndi inu, chifukwa kuti mkulu wake wafa, ndipo watsala iye yekha; ngati choipa chikamgwera iye m'njira m'mene mupitamo, inu mudzatsitsira ndi chisoni imvi zanga kumanda.


ndipo Israele anati, Chakwana; Yosefe mwana wanga akali ndi moyo; ndidzamuka ndikamuone iye ndisanafe.


Ndipo Israele anati kwa Yosefe, Sindinaganizira kuti ndiona nkhope yako: ndipo, taona, Mulungu wandionetsa ine mbeu zako zomwe.


Ndipo akulu a m'nyumba yake ananyamuka, naima pa iye, kuti akamuutse pansi; koma anakana, osafuna kudya nao.


Koma tsopano wafa, ndidzasaliranjinso kudya? Kodi ndikhoza kumbweza? Ine ndidzamuka kuli iye, koma iye sadzabweranso kwa ine.


Ndipo anauza Yowabu, Onani mfumu ilikulira misozi, nilira Abisalomu.


Ndipo Efuremu atate wao, anachita maliro masiku ambiri, ndi abale ake anadza kudzamtonthoza mtima.


Atamva tsono mabwenzi atatu a Yobu za choipa ichi chonse chidamgwera, anadza, yense kuchokera kwao, Elifazi wa ku Temani, ndi Bilidadi Msuki, ndi Zofari wa ku Naama, napangana kudzafika kumlirira ndi kumsangalatsa.


Tsiku la nsautso yanga ndinafuna Ambuye. Dzanja langa linatambalika usiku, losaleka; mtima wanga unakana kutonthozedwa.


Ndikumbukira Mulungu ndipo ndivutika; ndilingalira ndipo mzimu wanga ukomoka.


Chilichonse dzanja lako lichipeza kuchichita, uchichite ndi mphamvu yako; pakuti mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziwa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.


Atero Yehova: Mau a amveka mu Rama, maliro ndi kulira kwakuwawa, Rakele alinkulirira ana ake; akana kutonthozedwa mtima pa ana ake, chifukwa palibe iwo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa