Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Chivumbulutso 3:9 - Buku Lopatulika

9 Taona, ndikupatsa ena otuluka m'sunagoge wa Satana akudzinenera okha ali Ayuda, osakhala Ayuda, komatu anama; taona, ndidzawadzetsa alambire pa mapazi ako, nazindikire kuti Ine ndakukonda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Taona, ndikupatsa ena otuluka m'sunagoge wa Satana akudzinenera okha ali Ayuda, osakhala Ayuda, komatu anama; taona, ndidzawadzetsa alambire pa mapazi ako, nazindikire kuti Ine ndakukonda.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Alipo ena a mpingo wa Satana, amene sali Ayuda, koma amanama kuti ndi Ayuda. Iwoŵa ndidzaŵabweretsa kwa inu kuti adzadzigwetse kumapazi kwanu. Pamenepo adzadziŵa kuti ndimakukondani.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Amene ndi mpingo wa Satana, amene amadzitcha kuti ndi Ayuda pamene sali choncho, koma ndi onama, ndidzawabweretsa kwa inu ndi kuwagwetsa pansi pa mapazi anu kuti adzazindikire kuti ndimakukondani.

Onani mutuwo Koperani




Chivumbulutso 3:9
13 Mawu Ofanana  

Ndi m'maiko monse, ndi m'mizinda yonse, mudafika mau a mfumu ndi lamulo lake, Ayuda anali nako kukondwera ndi chimwemwe, madyerero ndi tsiku lokoma. Ndipo ambiri a mitundu ya anthu a m'dziko anasanduka Ayuda; pakuti kuopsa kwa Ayuda kudawagwera.


Ndipo anyamata ako onse awa adzanditsikira, nadzandigwadira, ndi kuti, Tulukani inu, ndi anthu onse akukutsatani; ndipo pambuyo pake ndidzatuluka. Ndipo anatuluka kwa Farao wakupsa mtima.


Pokhala iwe wa mtengo wapatali pamaso panga, ndi wolemekezeka, ndipo ndakukonda iwe; Ine ndidzakuombola ndi anthu, ndi kupereka anthu m'malo mwa moyo wako.


Atero Yehova, Ntchito ya Ejipito, ndi malonda a Kusi, ndi a Seba, amuna amsinkhu adzakugonjera, nadzakhala ako; nadzakutsata pambuyo m'maunyolo; adzakugonjera, nadzakugwira; adzakupembedza ndi kunena, Zoona Mulungu ali mwa iwe; ndipo palibenso wina, palibe Mulungu.


Ndipo mafumu adzakulera, ndi akazi ao aakulu adzakuyamwitsa; iwo adzakugwadira ndi nkhope zao zoyang'ana pansi, nadzaseteka fumbi la m'mapazi ako: ndipo iwe udzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndi iwo amene alindira Ine sadzakhala ndi manyazi.


Ndipo ana aamuna a iwo amene anavuta iwe adzafika, nadzakugwadira; ndipo iwo onse amene anakuchepetsa iwe adzagwadira kumapazi ako, nadzakutcha iwe, Mzinda wa Yehova, Ziyoni wa Woyera wa Israele.


Ine mwa iwo, ndi Inu mwa Ine, kuti akhale angwiro mwa mmodzi; kuti dziko lapansi lizindikire kuti Inu munandituma Ine, nimunawakonda iwo, monga momwe munakonda Ine.


Ndidziwa chisautso chako, ndi umphawi wako (komatu uli wachuma), ndi mwano wa iwo akunena za iwo okha kuti ali Ayuda, osakhala Ayuda, komatu sunagoge wa Satana.


Ndipo kudzali kuti yense wakusiyidwa wa m'banja lako adzabwera kwa iye nadzawerama ndi kupempha ndalama ndi chakudya, nadzati, Mundipatsetu ntchito ina ya wansembe, kuti ndikaone kakudya.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa