Tsono kunachitika, pakufikanso chaka Benihadadi anamemeza Aaramu nakwera ku Afeki kukaponyana ndi Aisraele.
1 Samueli 4:1 - Buku Lopatulika Ndipo mau a Samuele anafikira kwa Aisraele onse. Ndipo Aisraele anatuluka kukaponyana nkhondo ndi Afilisti, namanga zithando zao ku Ebenezeri; Afilistiwo namanga mu Afeki. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mau a Samuele anafikira kwa Aisraele onse. Ndipo Aisraele anatuluka kukaponyana nkhondo ndi Afilisti, namanga zithando zao ku Ebenezeri; Afilistiwo namanga m'Afeki. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsiku lina Aisraele adatuluka kukamenyana nkhondo ndi Afilisti. Adamanga zithando zankhondo ku Ebenezeri, ndipo Afilisti adamanga zithando zao ku Afeki. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo mawu a Samueli anafika kwa Aisraeli onse. Aisraeli anapita kukamenya nkhondo ndi Afilisti. Aisraeli anamanga misasa yawo ku Ebenezeri, ndipo Afilisti anamanga ku Afeki. |
Tsono kunachitika, pakufikanso chaka Benihadadi anamemeza Aaramu nakwera ku Afeki kukaponyana ndi Aisraele.
Ndipo otsalawo anathawira ku Afeki kumzinda, ndipo linga linawagwera anthu zikwi makumi awiri mphambu asanu ndi awiri amene adatsalawo. Ndipo Benihadadi anathawa, nalowa m'mzinda, m'chipinda cha m'katimo.
Muimirira inu nonse lero lino pamaso pa Yehova Mulungu wanu; mafumu anu, mafuko anu, akulu anu, ndi akapitao anu, amuna onse a Israele,
kumwera dziko lonse la Akanani, ndi Meara ndiwo wa Asidoni, mpaka ku Afeki, mpaka ku malire a Aamori;
koma lero inu mwakana Mulungu wanu amene anakupulumutsani yekha m'matsoka anu onse, ndi m'masautso anu; ndipo munanena naye, Koma mutipatse mfumu. Chifukwa chake tsono mudzionetse pamaso pa Yehova mafukomafuko, ndi magulumagulu.
Tsono Afilisti anasonkhanitsa makamu ao onse ku Afeki; ndipo Aisraele anamanga ku chitsime cha mu Yezireele.
Ndipo Yehova ananena ndi Samuele, Taona, ndidzachita mwa Israele choliritsa mwini khutu kwa munthu yense wakuchimva.
Ndipo Afilistiwo anandandalitsa nkhondo yao pa Aisraele; ndipo pokomana nkhondo Aisraele anakanthidwa ndi Afilisti. Ndipo anapha kuthengoko anthu zikwi zinai a khamu lao.
Ndipo Afilisti anatenga likasa la Mulungu, nachoka nalo ku Ebenezeri, napita ku Asidodi.
Pamenepo Samuele anatenga mwala nauimika pakati pa Mizipa ndi Sene, nautcha dzina lake Ebenezeri, nati, Kufikira pano Yehova anatithandiza.