1 Samueli 5 - Buku LopatulikaLikasa la Mulungu kunyumba ya Dagoni 1 Ndipo Afilisti anatenga likasa la Mulungu, nachoka nalo ku Ebenezeri, napita ku Asidodi. 2 Ndipo Afilistiwo anatenga likasa la Mulungu, nafika nalo kunyumba ya Dagoni, naliika pafupi ndi Dagoni. 3 Ndipo pakuuka a ku Asidodi mamawa taonani Dagoni adagwa pansi, nagona chafufumimba patsogolo pa likasa la Yehova. Ndipo iwo anatenga Dagoni namuimikanso m'malo mwake. 4 Ndipo m'mawa mwake polawirira, taonani, Dagoni adagwa pansi, nagona chafufumimba patsogolo pa likasa la Yehova; ndipo mutu wake ndi zikhato zonse ziwiri za manja ake zinagona zoduka pachiundo; Dagoni anatsala thupi lokha. 5 Chifukwa chake angakhale ansembe, angakhale ena akulowa m'nyumba ya Dagoni, palibe woponda pa chiundo cha Dagoni ku Asidodi, kufikira lero lino. Masauko a Afilisti chifukwa cha likasa 6 Koma Yehova anavuta iwo a ku Asidodi ndi dzanja lake, nawaononga, nawazunza ndi mafundo, mu Asidodi ndi m'midzi yake. 7 Ndipo pamene anthu a ku Asidodi anaona kuti nchomwecho, anati iwowa, Likasa la Mulungu wa Israele lisakhalitse ndi ife; popeza dzanja lake litiwawira ife, ndi Dagoni mulungu wathu. 8 Chifukwa chake anatumiza mithenga, nasonkhanitsa mafumu onse a Afilisti, nati Tichite nalo chiyani likasa la Mulungu wa Israele? Ndipo anati, Anyamule likasa la Mulungu kunka nalo ku Gati. Ndipo ananyamula likasalo la Mulungu wa Israele, napita nalo kumeneko. 9 Ndipo kunali atafika nalo, dzanja la Yehova linatsutsa mzindawo ndi kusautsa kwakukulu; ndipo anazunza anthu a mzindawo, aakulu ndi aang'ono; ndi mafundo anawabuka. 10 Chifukwa chake anatumiza likasa la Mulungu ku Ekeroni. Ndipo kunali pofika likasalo ku Ekeroni, a ku Ekeroni anafuula nati, Anadzatitulira likasa la Mulungu wa Israele, kutipha ife ndi ana athu. 11 Chifukwa chake anatumiza, nasonkhanitsa mafumu onse a Afilisti, ndipo iwowa anati, Chotsani likasa la Mulungu wa Israele, lipitenso kumalo kwake, kuti lingationonge ife, ndi anthu athu; pakuti kunali kusautsa koopsa m'mzinda monse; dzanja la Mulungu linavutadi pamenepo. 12 Ndipo amene anapanda kufa anagwidwa ndi mafundowo; ndi kulira kwa mzindawo kunakwera kumwamba. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi