Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 5:6 - Buku Lopatulika

6 Koma Yehova anavuta iwo a ku Asidodi ndi dzanja lake, nawaononga, nawazunza ndi mafundo, mu Asidodi ndi m'midzi yake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Koma Yehova anavuta iwo a ku Asidodi ndi dzanja lake, nawaononga, nawazunza ndi mafundo, m'Asidodi ndi m'milaga yake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Kenaka Chauta adalanga koopsa anthu a ku Asidodi. Iwowo pamodzi ndi anthu a m'dziko lozungulira adaŵalanga ndi mafundo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Yehova analanga koopsa anthu a ku Asidodi. Yehova anawawononga ndi kuwazunza ndi zithupsa Asidoniwa pamodzi ndi anthu a madera ozungulira.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 5:6
13 Mawu Ofanana  

ndipo zochuluka sizidzazindikirika chifukwa cha njala ikudza m'mbuyoyo, pakuti idzavuta.


Si ndizo chionongeko cha wosalungama, ndi tsoka la ochita mphulupulu?


Yehova asunga onse akukondana naye; koma oipa onse adzawaononga.


Yehova agwiriziza ofatsa; atsitsira oipa pansi.


Chifukwa usana ndi usiku dzanja lanu linandilemera ine; uwisi wanga unasandulika kuuma kwa malimwe.


Ndipo anapanda otsutsana naye kumbuyo; nawapereka akhale otonzeka kosatha.


taona, dzanja la Yehova lidzakhala pa zoweta zako za kubusa, pa akavalo, pa abulu, pa ngamira, pa ng'ombe, ndi pa zoweta zazing'ono ndi kalira woopsa.


Ndipo tsopano, taona, dzanja la Ambuye lili pa iwe, ndipo udzakhala wakhungu wosapenya dzuwa nthawi. Ndipo pomwepo lidamgwera khungu ndi mdima; ndipo anamukamuka nafuna wina womgwira dzanja.


Yehova adzakukanthani ndi zilombo za ku Ejipito, ndi nthenda yotuluka mudzi, ndi chipere, ndi mphere, osachira nazo.


Chifukwa chake anatumiza, nasonkhanitsa mafumu onse a Afilisti, ndipo iwowa anati, Chotsani likasa la Mulungu wa Israele, lipitenso kumalo kwake, kuti lingationonge ife, ndi anthu athu; pakuti kunali kusautsa koopsa m'mzinda monse; dzanja la Mulungu linavutadi pamenepo.


Ndipo pamene anthu a ku Asidodi anaona kuti nchomwecho, anati iwowa, Likasa la Mulungu wa Israele lisakhalitse ndi ife; popeza dzanja lake litiwawira ife, ndi Dagoni mulungu wathu.


Ndipo kunali atafika nalo, dzanja la Yehova linatsutsa mzindawo ndi kusautsa kwakukulu; ndipo anazunza anthu a mzindawo, aakulu ndi aang'ono; ndi mafundo anawabuka.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa