Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 5:3 - Buku Lopatulika

3 Ndipo pakuuka a ku Asidodi mamawa taonani Dagoni adagwa pansi, nagona chafufumimba patsogolo pa likasa la Yehova. Ndipo iwo anatenga Dagoni namuimikanso m'malo mwake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo pakuuka a ku Asidodi mamawa taonani Dagoni adagwa pansi, nagona chafufumimba patsogolo pa likasa la Yehova. Ndipo iwo anatenga Dagoni namuimikanso m'malo mwake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 M'maŵa mwake anthu a ku Asidodi atadzuka m'mamaŵa, adangoona Dagoni atagwa chafufumimba patsogolo pa Bokosi lachipanganolo. Apo anthuwo adatenga fanolo, naliikanso pamalo pake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Anthu a ku Asidodi atadzuka mmawa mwake, anangoona Dagoni atagwa pansi chafufumimba pamaso pa Bokosi la Yehova! Iwo anatenga Dagoni ndi kumuyimika pamalo pake.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 5:3
17 Mawu Ofanana  

Ndipo iwo anatenga ng'ombe ija adawapatsa, naikonza, naitana dzina la Baala, kuyambira m'mawa kufikira pausana, nati, Baala, timvereni ife. Koma panalibe mau kapena wovomereza. Ndipo anavinavina kuguwa adalimanga.


manja ali nao, koma osagwira; mapazi ali nao, koma osayenda; kapena sanena pammero pao.


Onse akutumikira fano losema, akudzitamandira nao mafano, achite manyazi: Mgwadireni Iye, milungu yonse inu.


Pakuti ndidzapita pakati padziko la Ejipito usiku womwewo, ndi kukantha ana oyamba onse m'dziko la Ejipito, anthu ndi zoweta; ndipo ndidzachita maweruzo pa milungu yonse ya Aejipito; Ine ndine Yehova.


Katundu wa Ejipito. Taonani, Yehova wakwera pamwamba pa mtambo wothamanga, nadza ku Ejipito; ndi mafano a Ejipito adzagwedezeka pakufika kwake, ndi mtima wa Ejipito udzasungunuka pakati pake.


Wosowa nsembe yoteroyo asankha mtengo umene sungavunde, iye adzisankhira yekha munthu mmisiri waluso, akonze fano losema, limene silisunthika.


Chotero mmisiri wa mitengo analimbikitsa wosula golide, ndi iye amene asalaza ndi nyundo anamlimbikitsa iye amene amenya posulira, nanena za kulumikiza ndi ntovu, Kuli kwabwino; ndipo iye akhomera fanolo misomali kuti lisasunthike.


Iwo amanyamula mlunguwu paphewa, nausenza, naukhazika m'malo mwake, nukhala chilili; pamalo pakepo sudzasunthika; inde, wina adzaufuulira, koma sungathe kuyankha, kapena kumpulumutsa m'zovuta zake.


Koma onse pamodzi apulukira ndi kupusa; mtengo ndiwo chilangizo, chopanda pake.


Yehova adzawakhalira woopsa; pakuti adzaondetsa milungu yonse ya padziko lapansi; ndipo adzamlambira Iye, yense pamalo pake, a m'zisumbu zonse za amitundu.


Ndipo mizimu yonyansa, m'mene inamuona Iye, inamgwadira, nifuula, niti, Inu ndinu Mwana wa Mulungu.


Ndipo likasa la Yehova linakhala ku dziko la Afilisti miyezi isanu ndi iwiri.


Chifukwa chake muzipanga zifanizo za mafundo anu, ndi zifanizo za mbewa zanu zimene ziipitsa dziko; ndipo muchitire ulemu Mulungu wa Israele; kuti kapena adzaleza dzanja lake pa inu, ndi pa milungu yanu, ndi padziko lanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa