Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 29:1 - Buku Lopatulika

1 Tsono Afilisti anasonkhanitsa makamu ao onse ku Afeki; ndipo Aisraele anamanga ku chitsime cha mu Yezireele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Tsono Afilisti anasonkhanitsa makamu ao onse ku Afeki; ndipo Aisraele anamanga ku chitsime cha m'Yezireele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Afilisti adasonkhanitsa magulu ao ankhondo ku Afeki. Nawonso Aisraele adamanga zithando zankhondo pa chitsime cha ku Yezireele.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Afilisti anasonkhanitsa asilikali awo onse ku Afeki, ndipo Israeli anamanga misasa yawo pa chitsime cha Yezireeli.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 29:1
20 Mawu Ofanana  

namlonga ufumu wa pa Giliyadi ndi Aasiriya ndi Yezireele ndi Efuremu ndi Benjamini ndi Aisraele onse.


Koma pamene Afilisti anamva kuti adamdzoza Davide mfumu ya Israele, Afilisti onse anakwera kukafuna Davide; ndipo Davide anachimva natsikira kungaka kuja.


Ndipo otsalawo anathawira ku Afeki kumzinda, ndipo linga linawagwera anthu zikwi makumi awiri mphambu asanu ndi awiri amene adatsalawo. Ndipo Benihadadi anathawa, nalowa m'mzinda, m'chipinda cha m'katimo.


Ndipo zitatha izi, kunaoneka zotere: Naboti wa ku Yezireele anali ndi munda wampesa, unali mu Yezireelemo, m'mbali mwa nyumba ya Ahabu mfumu ya ku Samariya.


Ndipo za Yezebele yemwe Yehova ananena, nati, Agalu adzadya Yezebele ku linga la Yezireele.


Ndipo pofika Yehu ku Yezireele, Yezebele anamva, nadzikometsera m'maso, naluka tsitsi lake, nasuzumira pazenera.


Nabwerera iwo, namfotokozera. Nati iye, Ndiwo mau a Yehova ananenawo mwa mtumiki wake Eliya wa ku Tisibe, ndi kuti, Pa munda wa Yezireele agalu adzadya mnofu wa Yezebele;


Gebala ndi Amoni ndi Amaleke; Filistiya, pamodzi ndi iwo okhala mu Tiro.


mfumu ya ku Afeki, imodzi; mfumu ya ku Lasaroni, imodzi;


Ndipo ana a Yosefe anati, Ku phiriko sikudzatifikira; ndipo Akanani onse akukhala m'dziko la chigwa ali nao magaleta achitsulo, iwo akukhala mu Beteseani, ndi midzi yake ndi iwo omwe akukhala m'chigwa cha Yezireele.


Ndi malire ao anali ku Yezireele, ndi Kesuloti, ndi Sunemu;


Uma womwe ndi Afeki, ndi Rehobu; mizinda makumi awiri mphambu iwiri ndi midzi yao.


Pamenepo Amidiyani onse ndi Aamaleke ndi ana a kum'mawa anasonkhana pamodzi naoloka, namanga misasa m'chigwa cha Yezireele.


Pamenepo Yerubaala, ndiye Gideoni, ndi anthu onse okhala naye anauka mamawa, namanga misasa pa chitsime cha Harodi, ndi misasa ya Midiyani inali kumpoto kwao, paphiri la More m'chigwa.


nabwera nazo kwa Saulo ndi kwa anyamata ake; nadya iwowa. Atatero ananyamuka, nachoka usiku womwewo.


Ndipo Afilisti anasonkhana, nadza namanga misasa ku Sunemu; ndipo Saulo anasonkhanitsa Aisraele onse, namanga iwo ku Gilibowa.


Ndipo mau a Samuele anafikira kwa Aisraele onse. Ndipo Aisraele anatuluka kukaponyana nkhondo ndi Afilisti, namanga zithando zao ku Ebenezeri; Afilistiwo namanga mu Afeki.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa