Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Samueli 4:1 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Ndipo mawu a Samueli anafika kwa Aisraeli onse. Aisraeli anapita kukamenya nkhondo ndi Afilisti. Aisraeli anamanga misasa yawo ku Ebenezeri, ndipo Afilisti anamanga ku Afeki.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

1 Ndipo mau a Samuele anafikira kwa Aisraele onse. Ndipo Aisraele anatuluka kukaponyana nkhondo ndi Afilisti, namanga zithando zao ku Ebenezeri; Afilistiwo namanga mu Afeki.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo mau a Samuele anafikira kwa Aisraele onse. Ndipo Aisraele anatuluka kukaponyana nkhondo ndi Afilisti, namanga zithando zao ku Ebenezeri; Afilistiwo namanga m'Afeki.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Tsiku lina Aisraele adatuluka kukamenyana nkhondo ndi Afilisti. Adamanga zithando zankhondo ku Ebenezeri, ndipo Afilisti adamanga zithando zao ku Afeki.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 4:1
14 Mawu Ofanana  

Chaka chinacho Beni-Hadadi anasonkhanitsa Aaramu, napita ku Afeki kukamenyana ndi Israeli.


Ena onse otsala anathawira ku Afeki, kumene khoma linagwera anthu 27,000. Ndipo Beni-Hadadi anathawira mu mzinda, nakabisala mʼchipinda chamʼkati.


Agebala, Aamoni ndi Aamaleki, Afilisti, pamodzi ndi anthu a ku Turo.


Lero lino nonse mukuyima pamaso pa Yehova Mulungu wanu, atsogoleri a mafuko anu, akuluakulu ndi nduna zanu, ndi amuna ena onse a mu Israeli,


mfumu ya Afeki imodzi mfumu ya Lasaroni imodzi


Dziko lina la Akanaani ndi Ameara limene lili mʼmanja mwa Asidoni mpaka ku Afeki, dziko limene linachitana malire ndi dziko la Aamori.


Yanumu, Beti-Tapuwa, Afeki


Uma, Afeki ndi Rehobu. Mizinda yonse inalipo 22 pamodzi ndi midzi yake.


Koma lero mwamukana Mulungu wanu amene amakupulumutsani mʼmavuto anu onse ndi mʼzowawa zanu. Ndipo mukuti, ‘Ayi, koma mutipatse mfumu yotilamulira.’ Tsopanotu sonkhanani pamaso pa Yehova mwa mafuko ndi mabanja anu.”


Afilisti anasonkhanitsa asilikali awo onse ku Afeki, ndipo Israeli anamanga misasa yawo pa chitsime cha Yezireeli.


Ndipo Yehova anati kwa Samueli, “Taona, patsala pangʼono kuti ndichite chinthu china mu Israeli chimene chidzadabwitsa aliyense amene adzamve.


Afilisti anandanda kuyangʼana Aisraeli nayamba kumenyana. Nkhondo inakula ndipo Afilisti anagonjetsa Aisraeli napha anthu 4,000 pa malo a nkhondopo.


Afilisti atalanda Bokosi la Mulungu lija, analitenga kuchoka ku Ebenezeri kupita ku Asidodi.


Kenaka Samueli anatenga mwala nawuyika pakati pa Mizipa ndi Seni. Iye anawutcha Ebenezeri, popeza anati, “Yehova watithandiza mpaka pano.”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa