Yoswa 15 - Buku LopatulikaMalire a Yuda 1 Ndipo gawo la fuko la ana a Yuda monga mwa mabanja ao linafikira malire a Edomu, ku chipululu cha Zini kumwera, ku malekezero a kumwera. 2 Ndi malire ao a kumwera, anayambira ku malekezero a Nyanja ya Mchere, ku nyondo yoloza kumwera; 3 natuluka kumwera kwa chikweza cha Akarabimu, napitirira ku Zini, nakwera kumwera kwa Kadesi-Baranea, napitirira ku Hezironi, nakwera ku Adara, nazungulira ku Karika; 4 napitirira ku Azimoni, natuluka ku mtsinje wa Ejipito; ndi malekezero a malirewa anali ku Nyanja Yaikulu; awa ndi malire anu a kumwera. 5 Ndi malire a kum'mawa ndiwo Nyanja ya Mchere, mpaka mathiriro ake a Yordani. Ndi malire a kumpoto anayambira nyondo ya nyanja ku mathiriro a Yordani; 6 nakwera malire kunka ku Betehogila, napitirira kumpoto kwa Betaraba; nakwera malire kunka ku mwala wa Bohani mwana wa Rubeni; 7 nakwera malire kunka ku Debiri, kuchokera ku chigwa cha Akori, ndi kumpoto kupenyera Giligala ndiko kundunji kwa chikweza cha Adumimu, ndiko kumwera kwa mtsinje; napitirira malire kunka ku madzi a Enisemesi, ndi matulukiro ake anali ku Enirogele; 8 nakwera malire kunka ku chigwa cha mwana wa Hinomu, kumbali kwa Ayebusi, kumwera, ndiko Yerusalemu; nakwera malire kunka kumwamba kwa phiri lokhala patsogolo pa chigwa cha Hinomu kumadzulo, ndilo ku mathero ake a chigwa cha Refaimu kumpoto. 9 Ndipo analemba malire kuyambira pamwamba paphiri mpaka chitsime cha madzi cha Nefitowa, natulukira malire kumizinda ya phiri la Efuroni; ndipo analemba malire kunka ku Baala, ndiwo Kiriyati-Yearimu. 10 Ndipo malire anazungulira kuyambira ku Baala kunka kumadzulo, kuphiri la Seiri, napitirira kumbali kwa phiri la Yearimu kumpoto, ndilo Kesaloni, natsikira ku Betesemesi, napitirira ku Timna; 11 natuluka malire kunka ku mbali ya Ekeroni kumpoto; ndipo analemba malire kunka ku Sikeroni, napitirira kuphiri la Baala, natuluka ku Yabinele; ndipo matulukiro a malire anali kunyanja. 12 Ndi malire a kumadzulo anali ku Nyanja Yaikulu ndiwo malire ake. Awa ndi malire a ana a Yuda pozungulira monga mwa mabanja ao. 13 Koma Yoswa anampatsa Kalebe mwana wa Yefune gawo mwa ana a Yuda, monga Yehova adamlamulira, ndiwo mudzi wa Araba, ndiye atate wa Anaki, ndiwo Hebroni. 14 Ndipo Kalebe anaingitsako ana aamuna atatu a Anaki, ndiwo Sesai, ndi Ahimani, ndi Talimai, ana a Anaki. 15 Nakwera komweko kunka kwa nzika za Debiri; koma kale dzina la Debiri ndilo Kiriyati-Sefere. 16 Ndipo Kalebe anati, Iye amene akantha Kiriyati-Sefere, naulanda, yemweyo ndidzampatsa Akisa mwana wanga akhale mkazi wake. 17 Ndipo Otiniyele mwana wa Kenazi, mbale wake wa Kalebe, anaulanda; ndipo anampatsa Akisa mwana wake akhale mkazi wake. 18 Ndipo kunali, m'mene anamdzera, anamkangamiza mwamuna wake kuti apemphe atate wake ampatse munda; ndipo anatsika pabulu; pamenepo Kalebe ananena naye, Ufunanji? 19 Nati iye, Mundipatse dalitso; popeza mwandipatsa dziko la kumwera, ndipatseninso zitsime za madzi. Pamenepo anampatsa zitsime za kumtunda, ndi zitsime za kunsi. 20 Ichi ndi cholowa cha fuko la ana a Yuda monga mwa mabanja ao. 21 Ndipo mizinda ya ku malekezero a fuko la ana a Yuda ku malire a Edomu, kumwera ndiwo, Kabizeeli ndi Edere, ndi Yaguru; 22 ndi Kina ndi Dimona, ndi Adada; 23 ndi Kedesi, ndi Hazori, ndi Itinani; 24 Zifi ndi Telemu ndi Bealoti; 25 ndi Hazori-Hadata, ndi Keriyoti-Hezironi, ndiwo Hazori; 26 Amama ndi Sema ndi Molada; 27 ndi Hazara-Gada, ndi Hesimoni, ndi Betepeleti; 28 ndi Hazara-Suwala, ndi Beereseba, ndi Biziyotiya; 29 Baala, ndi Iyimu, ndi Ezemu; 30 ndi Elitoladi, ndi Kesili ndi Horoma; 31 ndi Zikilagi, ndi Madimana ndi Sanisana; 32 ndi Lebaoti, ndi Silihimu, ndi Aini ndi Rimoni; mizinda yonse ndiyo makumi awiri kudza isanu ndi inai; pamodzi ndi midzi yao. 33 Ku chigwa, Esitaoli, ndi Zora ndi Asina; 34 ndi Zanowa, ndi Enganimu, Tapuwa, ndi Enamu; 35 Yaramuti, ndi Adulamu, Soko, ndi Azeka; 36 ndi Saaraimu, ndi Aditaimu, ndi Gedera, ndi Gederotaimu; mizinda khumi ndi inai pamodzi ndi midzi yao. 37 Zenani, ndi Hadasa, ndi Megidali-Gadi; 38 ndi Dileani, ndi Mizipa, ndi Yokotele; 39 Lakisi ndi Bozikati ndi Egiloni; 40 ndi Kaboni, ndi Lahamasi, ndi Kitilisi; 41 ndi Gederoti, Betedagoni, ndi Naama, ndi Makeda; mizinda khumi ndi isanu ndi umodzi pamodzi ndi midzi yao. 42 Libina ndi Eteri ndi Asani; 43 ndi Ifuta ndi Asina ndi Nezibu; 44 ndi Keila ndi Akizibu, ndi Maresa; mizinda isanu ndi inai pamodzi ndi midzi yao. 45 Ekeroni pamodzi ndi mizinda yake ndi midzi yao; 46 kuyambira ku Ekeroni mpaka kunyanja, yonse ya ku mbali ya Asidodi, pamodzi ndi midzi yao. 47 Asidodi, mizinda yake ndi midzi yake; Gaza, mizinda yake ndi midzi yake; mpaka mtsinje wa Ejipito, ndi Nyanja Yaikulu ndi malire ake. 48 Ndi kumapiri Samiri, ndi Yatiri, ndi Soko; 49 ndi Dana, ndi Kiriyati-Sana, ndiwo Debiri; 50 ndi Anabu, ndi Esitemowa, ndi Animu; 51 ndi Goseni, ndi Holoni, ndi Gilo; mizinda khumi ndi umodzi pamodzi ndi midzi yao. 52 Arabu, ndi Duma, ndi Esani; 53 ndi Yanimu, ndi Betetapuwa, ndi Afeka; 54 ndi Humata, ndi Kiriyati-Ariba, ndiwo Hebroni, ndi Ziyori; mizinda isanu ndi inai pamodzi ndi midzi yao. 55 Maoni, Karimele, ndi Zifi, ndi Yuta; 56 ndi Yezireele, ndi Yokodeamu, ndi Zanowa; 57 Kaini, Gibea ndi Timna; mizinda khumi pamodzi ndi midzi yao. 58 Halahulu, Betezuri, ndi Gedori, 59 ndi Maarati, ndi Betanoti, ndi Elitekoni; mizinda isanu ndi umodzi pamodzi ndi midzi yao. 60 Kiriyati-Baala, ndiwo Kiriyati-Yearimu ndi Raba; mizinda iwiri pamodzi ndi midzi yao. 61 M'chipululu, Betaraba, Midini, ndi Sekaka; 62 ndi Nibisani, ndi Mzinda wa Mchere, ndi Engedi; mizinda isanu ndi umodzi pamodzi ndi midzi yao. 63 Koma ana a Yuda sanakhoze kuingitsa Ayebusi, nzika za Yerusalemu: m'mwemo Ayebusi anakhala pamodzi ndi ana a Yuda, ku Yerusalemu, mpaka lero lino. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi