Yoswa 19 - Buku LopatulikaMalire a Simeoni 1 Ndipo maere achiwiri anamtulukira Simeoni, fuko la ana a Simeoni monga mwa mabanja ao; ndi cholowa chao chinali pakati pa cholowa cha ana a Yuda. 2 Ndipo anali nacho cholowa chao Beereseba, kapena Sheba, ndi Molada; 3 ndi Hazara-Suwala, ndi Bala, ndi Ezemu; 4 ndi Elitoladi, ndi Betuli, ndi Horoma; 5 ndi Zikilagi, ndi Betemara-Kaboti, ndi Hazara-Susa: 6 ndi Betelebaoti, ndi Saruheni; mizinda khumi ndi itatu ndi midzi yao; 7 Aini, Rimoni ndi Eteri ndi Asani; mizinda inai ndi midzi yao; 8 ndi midzi yonse yozungulira mizinda iyi mpaka Baalati-Bere ndiwo Rama kumwera. Ndicho cholowa cha fuko la ana a Simeoni, monga mwa mabanja ao. 9 M'gawo la ana a Yuda muli cholowa cha ana a Simeoni; popeza gawo la ana a Yuda linawachulukira; chifukwa chake ana a Simeoni anali nacho cholowa pakati pa cholowa chao. Malire a Zebuloni 10 Ndipo maere achitatu anakwerera ana a Zebuloni monga mwa mabanja ao; ndi malire a cholowa chao anafikira ku Saridi; 11 nakwera malire ao kunka kumadzulo ndi ku Mareyala nafikira ku Dabeseti, nafikira ku mtsinje wa patsogolo pa Yokoneamu; 12 ndi kuchokera ku Saridi anazungulira kunka kum'mawa kumatulukira dzuwa, mpaka malire a Kisiloti-Tabori; natuluka kunka ku Daberati, nakwera ku Yafiya; 13 ndi pochoka pamenepo anapitirira kunka kum'mawa ku Gatihefere, ku Etikazini; natuluka ku Rimoni umene ulembedwa mpaka ku Neya, 14 nauzungulira malire kumpoto, kunka ku Hanatoni; ndi matulukiro ake anali ku chigwa cha Ifutahele; 15 ndi Katati, ndi Nahalala ndi Simironi, ndi Idala ndi Betelehemu: mizinda khumi ndi iwiri ndi midzi yao. 16 Ichi ndi cholowa cha ana a Zebuloni monga mwa mabanja ao, mizinda iyi ndi midzi yao. Malire a Isakara 17 Maere achinai anamtulukira Isakara, kunena za ana a Isakara monga mwa mabanja ao. 18 Ndi malire ao anali ku Yezireele, ndi Kesuloti, ndi Sunemu; 19 ndi Hafaraimu, ndi Siyoni, ndi Anaharati; 20 ndi Rabiti ndi Kisiyoni, ndi Ebezi; 21 ndi Remeti ndi Enganimu ndi Enihada, ndi Betepazezi; 22 ndi malire anafikira ku Tabori, ndi Sahazuma, ndi Betesemesi; ndi matulukiro a malire ao anali ku Yordani; mizinda khumi ndi isanu ndi umodzi ndi midzi yao. 23 Ichi ndi cholowa cha fuko la ana a Isakara, monga mwa mabanja ao, mizinda ndi midzi yao. Malire a Asere 24 Ndipo maere achisanu analitulukira fuko la ana a Asere monga mwa mabanja ao. 25 Ndi malire ao ndiwo Helekati, ndi Hali, ndi Beteni ndi Akisafu; 26 ndi Alamumeleki, ndi Amada, ndi Misala; nafikira ku Karimele kumadzulo ndi ku Sihori-Libinati; 27 nazungulira kotulukira dzuwa ku Betedagoni, nafikira ku Zebuloni ndi ku chigwa cha Ifutahele, kumpoto ku Betemeke, ndi Neiyeli; natulukira ku Kabulu kulamanzere, 28 ndi Ebroni, ndi Rehobu, ndi Hamoni, ndi Kana, mpaka ku Sidoni wamkulu; 29 nazungulira malire kunka ku Rama, ndi kumzinda wa linga la Tiro; nazungulira malire kunka ku Hosa; ndi matulukiro ake anali kunyanja, kuchokera ku Mahalabu mpaka ku Akizibu; 30 Uma womwe ndi Afeki, ndi Rehobu; mizinda makumi awiri mphambu iwiri ndi midzi yao. 31 Ichi ndi cholowa cha fuko la ana a Asere monga mwa mabanja ao, mizinda iyi ndi midzi yao. Malire a Nafutali 32 Maere achisanu ndi chimodzi anatulukira ana a Nafutali, ana a Nafutali monga mwa mabanja ao. 33 Ndipo malire ao anayambira ku Helefe ku thundu wa ku Zaananimu, ndi Adami-Nekebu, ndi Yabinele, mpaka ku Lakumu; ndi matulukiro ake anali ku Yordani; 34 nazungulira malire kunka kumadzulo ku Azinoti-Tabori, natulukira komweko kunka ku Hukoku; nafikira ku Zebuloni kumwera, nafikira ku Asere kumadzulo, ndi ku Yuda pa Yordani kum'mawa. 35 Ndipo mizinda yamalinga ndiyo Zidimu, Zeri, ndi Hamati, Rakati, ndi Kinereti; 36 ndi Adama, ndi Rama, ndi Hazori; 37 ndi Kedesi, ndi Ederei, ndi Enihazori; 38 ndi Yironi, ndi Migidalele, Horemu, ndi Betanati, ndi Betesemesi; mizinda khumi ndi isanu ndi inai, ndi midzi yao. 39 Ichi ndi cholowa cha fuko la ana a Nafutali, monga mwa mabanja ao, mizinda ndi midzi yao. Malire a Dani 40 Maere achisanu ndi chiwiri anatulukira fuko la ana a Dani, monga mwa mabanja ao. 41 Ndipo malire a cholowa chao anali Zora, ndi Esitaoli, ndi Irisemesi; 42 Saalabini, ndi Ayaloni ndi Itila; 43 ndi Eloni ndi Timna ndi Ekeroni; 44 ndi Eliteke, ndi Gibetoni, ndi Baalati; 45 ndi Yehudi, ndi Beneberaki, ndi Gatirimoni; 46 ndi Meyarikoni, ndi Rakoni, ndi malire pandunji pa Yopa. 47 Koma malire a ana a Dani anatuluka kupitirira iwowa; pakuti ana a Dani anakwera nathira nkhondo ku Lesemu, naulanda naukantha ndi lupanga lakuthwa, naulandira, nakhala m'mwemo, nautcha Lesemu, Dani; ndilo dzina la Dani atate wao. 48 Ichi ndi cholowa cha fuko la ana a Dani, monga mwa mabanja ao, mizinda iyi ndi midzi yao. Cholowa cha Yoswa 49 Ndipo atatha kuligawa dziko likhale cholowa chao monga mwa malire ake, ana a Israele anapatsa Yoswa mwana wa Nuni cholowa pakati pao; 50 monga mwa lamulo la Yehova anampatsa mzinda umene anawapempha, ndiwo Timnati-Sera, ku mapiri a Efuremu; ndipo anamanga mzindawo nakhala m'mwemo. 51 Izi ndizo zolowa anazigawa Eleazara wansembe, ndi Yoswa mwana wa Nuni, ndi akulu a nyumba za atate a mafuko a ana a Israele, zikhale zaozao, ndi kulota maere ku Silo pamaso pa Yehova ku khomo la chihema chokomanako. Momwemo anatha kuligawa dziko. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi