Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




1 Samueli 16:13 - Buku Lopatulika

Pamenepo Samuele anatenga nyanga ya mafuta, namdzoza pakati pa abale ake; ndipo mzimu wa Yehova unalimbika pa Davide kuyambira tsiku lomweli. Ndipo Samuele ananyamuka, nanka ku Rama.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Pamenepo Samuele anatenga nyanga ya mafuta, namdzoza pakati pa abale ake; ndipo mzimu wa Yehova unalimbika pa Davide kuyambira tsiku lomweli. Ndipo Samuele ananyamuka, nanka ku Rama.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Samuele adatenga nsupa ya mafuta, namdzoza pamaso pa abale ake. Ndipo mzimu wa Chauta udamloŵa Davide mwamphamvu kuyambira tsiku limenelo mpaka m'tsogolo mwake. Pambuyo pake Samuele adanyamuka napita ku Rama.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Samueli anatenga botolo la mafuta ndi kumudzoza pamaso pa abale ake, ndipo Mzimu wa Yehova unabwera mwamphamvu pa Davide kuyambira tsiku limenelo mpaka mʼtsogolo. Pambuyo pake Samueli anabwerera ku Rama.

Onani mutuwo



1 Samueli 16:13
27 Mawu Ofanana  

Ndipo Natani ananena kwa Davide, Munthuyo ndi inu nomwe. Atero Yehova, Mulungu wa Israele, Ndinakudzoza ukhale mfumu ya Israele, ndinakupulumutsa m'dzanja la Saulo;


Ndipo anthu Ayuda anabwera namdzoza Davide pomwepo akhale mfumu ya nyumba ya Yuda. Ndipo wina anauza Davide kuti, Anthu a ku Yabesi-Giliyadi ndiwo amene anamuika Saulo.


Ndipo mau otsiriza a Davide ndi awa: Atero Davide mwana wa Yese, atero munthu wokwezedwa, ndiye wodzozedwa wa Mulungu wa Yakobo, ndi mwini nyimbo yokoma ya Israele.


Chomwecho akulu onse a Israele anadza kwa mfumu ku Hebroni; ndipo mfumu Davide anapangana nao pangano ku Hebroni pamaso pa Yehova; ndipo anamdzoza Davide mfumu ya Israele.


Nanyamuka, nalowa m'nyumba; ndipo anatsanulira mafutawo pamutu pake, nanena naye, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Ndakudzoza ukhale mfumu ya pa anthu a Yehova, ndiwo Aisraele.


Akulu onse omwe a Israele anadza kwa mfumu ku Hebroni; ndipo Davide anapangana nao pangano ku Hebroni pamaso pa Yehova; ndipo anamdzoza Davide akhale mfumu ya Israele monga mwa mau a Yehova, ndi dzanja la Samuele.


Ndapeza Davide mtumiki wanga; ndamdzoza mafuta anga oyera.


Amene dzanja langa lidzakhazikika naye; inde mkono wanga udzalimbitsa.


Pamenepo ndidzatsika ndi kulankhula nawe komweko; ndipo ndidzatengako mzimu uli pa iwe, ndi kuika pa iwowa; adzakuthandiza kusenza katundu wa anthu awa, kuti usasenze wekha.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Utenge Yoswa mwana wa Nuni, ndiye munthu mwa iye muli mzimu, nuike dzanja lako pa iye;


Pakuti Iye amene Mulungu anamtuma alankhula mau a Mulungu; pakuti sapatsa Mzimu ndi muyeso.


Ndipo m'mene atamchotsa iye, anawautsira Davide akhale mfumu yao; amenenso anamchitira umboni, nati, Ndapeza Davide, mwana wa Yese, munthu wa pamtima panga, amene adzachita chifuniro changa chonse.


Mwakonda chilungamo, ndi kudana nacho choipa; mwa ichi Mulungu, ndiye Mulungu wanu, wakudzozani ndi mafuta a chikondwerero chenicheni koposa anzanu.


Ndipo ndinene chiyaninso? Pakuti idzandiperewera nthawi ndifotokozere za Gideoni, Baraki, Samisoni, Yefita; za Davide, ndi Samuele ndi aneneri;


Pamenepo mzimu wa Yehova unamdzera Yefita, napitira iye ku Giliyadi, ndi Manase, napitira ku Mizipa wa Giliyadi, ndi kuchokera ku Mizipa wa Giliyadi anapitira kwa ana a Amoni.


Ndipo mzimu wa Yehova unayamba kumfulumiza mtima ku misasa ya Dani pakati pa Zora ndi Esitaoli.


Ndipo unamgwera iye kolimba mzimu wa Yehova, naung'amba monga akadang'amba mwanawambuzi, wopanda kanthu m'dzanja lake; koma sanauze atate wake kapena amai wake chimene adachichita.


Ndipo unamdzera mzimu wa Yehova, iye naweruza Israele, natuluka kunkhondo; napereka Yehova Kusani-Risataimu mfumu ya Mesopotamiya m'dzanja lake; ndi dzanja lake linamgonjetsa Kusani-Risataimu.


Ndipo iwo anauka mamawa, nalambira pamaso pa Yehova, nabwerera, nafikanso kwao ku Rama; ndipo Elikana anadziwa mkazi wake Hana, Yehova namkumbukira iye.


Pamenepo Samuele anatenga nsupa ya mafuta, nawatsanulira pamutu pake, nampsompsona iye, nati, Sanakudzozeni ndi Yehova kodi, Mukhale mfumu ya pa cholowa chake?


ndipo Mzimu wa Yehova udzagwera inu kolimba, nanunso mudzanenera pamodzi nao, nimudzasandulika munthu wina.


Ndipo mzimu wa Mulungu unamgwera Saulo mwamphamvu, pamene anamva mau awa, ndi mkwiyo wake unayaka kwambiri.


Ndipo mnyamata wake wina anayankha, nati, Taonani, ine ndaona mwana wa Yese wa ku Betelehemu, ndiye wanthetemya wodziwa kuimbira, ndipo ali wa mtima wolimba ndi woyenera nkhondo, ndiponso ali wochenjera manenedwe ake; ndiye munthu wokongola, ndipo Yehova ali naye.


Ndipo Saulo anaopa Davide chifukwa Yehova anali naye, koma adamchokera Saulo.


Ndipo ndidzadziukitsira wansembe wokhulupirika, amene adzachita monga chimene chili mumtima mwanga ndi m'chifuniro changa; ndipo ndidzammangira nyumba yokhazikika, ndipo iyeyu adzayenda pamaso pa wodzozedwa wanga masiku onse.