1 Samueli 2:35 - Buku Lopatulika35 Ndipo ndidzadziukitsira wansembe wokhulupirika, amene adzachita monga chimene chili mumtima mwanga ndi m'chifuniro changa; ndipo ndidzammangira nyumba yokhazikika, ndipo iyeyu adzayenda pamaso pa wodzozedwa wanga masiku onse. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201435 Ndipo ndidzadziukitsira wansembe wokhulupirika, amene adzachita monga chimene chili mumtima mwanga ndi m'chifuniro changa; ndipo ndidzammangira nyumba yokhazikika, ndipo iyeyu adzayenda pamaso pa wodzozedwa wanga masiku onse. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa35 Pambuyo pake ndidzasankha wansembe wokhulupirika amene adzachita zinthu pomvera zimene mtima wanga ufuna ndiponso potsata maganizo anga. Ndidzammangira banja lolimba, ndipo adzatumikira pamaso pa wodzozedwa wanga nthaŵi zonse. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero35 Pambuyo pake ndidzasankha wansembe wokhulupirika, amene adzachita zimene zili mu mtima ndi mʼmaganizo mwanga. Ndidzakhazikitsa banja lako kolimba ndipo adzatumikira pamaso pa wodzozedwa wanga nthawi zonse. Onani mutuwo |
Ndipo kudzakhala kuti ukadzamvera iwe zonse ndikulamulirazo, nukadzayenda m'njira zanga ndi kuchita chilungamo pamaso panga, kusunga malemba anga ndi malamulo anga, monga anatero Davide mtumiki wanga pamenepo Ine ndidzakhala ndi iwe, ndidzakumangira ndi kukukhazikitsira nyumba, monga ndinammangira Davide, ndipo ndidzakupatsa iwe Israele.
Ndikalipo ine; chitani umboni wonditsutsa pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa wodzozedwa wake; ndinalanda ng'ombe ya yani? Kapena ndinalanda bulu wa yani? Ndinanyenga yani? Ndinasutsa yani? Ndinalandira m'manja mwa yani chokometsera mlandu kutseka nacho maso anga? Ngati ndinatero ndidzachibwezera kwa inu.