Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 2:36 - Buku Lopatulika

36 Ndipo kudzali kuti yense wakusiyidwa wa m'banja lako adzabwera kwa iye nadzawerama ndi kupempha ndalama ndi chakudya, nadzati, Mundipatsetu ntchito ina ya wansembe, kuti ndikaone kakudya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

36 Ndipo kudzali kuti yense wakusiyidwa wa m'banja lako adzabwera kwa iye nadzawerama ndi kupempha ndalama ndi chakudya, nadzati, Mundipatsetu ntchito ina ya wansembe, kuti ndikaona kakudya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

36 Apo aliyense amene adzatsale pabanja pako adzabwera kudzampempha iyeyo tindalama kapena kachakudya. Adzanena kuti, “Mundilole ndizithandizako ansembe, kuti ndipezeko kanthu kakudya.” ’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

36 Ndipo aliyense wotsala wa banja lako adzabwera ndi kugwada pamaso pake kupempha ndalama kapena chakudya.’ Adzati, ‘Chonde ndiloleni kuti ndizithandizako pa ntchito iliyonse ya unsembe kuti ndipeze chakudya.’ ”

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 2:36
9 Mawu Ofanana  

Motero Solomoni anachotsa Abiyatara asakhalenso wansembe wa Yehova, kuti akakwaniritse mau a Yehova amene aja adalankhula ku Silo za mbumba ya Eli.


Koma ansembe a misanje sanakwere kudza ku guwa la nsembe la Yehova ku Yerusalemu; koma anadya mkate wopanda chotupitsa pakati pa abale ao.


Oipa amagwadira abwino, ndi ochimwa pa makomo a olungama.


Mukutinso, Taonani, ncholemetsa ichi! Ndipo mwachipeputsa, ati Yehova wa makamu; ndipo mwabwera nazo zofunkha, ndi zotsimphina, ndi zodwala; momwemo mubwera nayo nsembe; kodi ndiyenera kuilandira kudzanja lanu? Ati Yehova.


Nanena naye Mika, Khalitsa nane, nukhale atate wanga, ndi wansembe wanga, ndipo ndidzakupatsa ndalama khumi pachaka, ndi chovala chofikira, ndi zakudya zako. Nalowa Mleviyo.


Ndipo ndidzadziukitsira wansembe wokhulupirika, amene adzachita monga chimene chili mumtima mwanga ndi m'chifuniro changa; ndipo ndidzammangira nyumba yokhazikika, ndipo iyeyu adzayenda pamaso pa wodzozedwa wanga masiku onse.


Ndipo mwanayo Samuele anatumikira Yehova pamaso pa Eli. Ndipo masiku aja mau a Yehova anamveka kamodzikamodzi; masomphenya sanaonekeoneke.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa