Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Mbiri 11:3 - Buku Lopatulika

3 Akulu onse omwe a Israele anadza kwa mfumu ku Hebroni; ndipo Davide anapangana nao pangano ku Hebroni pamaso pa Yehova; ndipo anamdzoza Davide akhale mfumu ya Israele monga mwa mau a Yehova, ndi dzanja la Samuele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Akulu onse omwe a Israele anadza kwa mfumu ku Hebroni; ndipo Davide anapangana nao pangano ku Hebroni pamaso pa Yehova; ndipo anamdzoza Davide akhale mfumu ya Israele monga mwa mau a Yehova, ndi dzanja la Samuele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Choncho atsogoleri onse a Aisraele adadza kwa mfumu ku Hebroni. Tsono Davide adachita nawo chipangano pamaso pa Chauta ku Hebroniko, ndipo anthuwo adamdzoza Davideyo kuti akhale mfumu ya Aisraele onse, potsata mau a Chauta ochokera m'kamwa mwa Samuele.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Akuluakulu onse a Israeli atafika kwa Mfumu Davide ku Hebroni, iye anachita nawo pangano pamaso pa Yehova, ndipo anamudzoza Davide kukhala mfumu ya Israeli, monga momwe Yehova analonjezera kudzera mwa Samueli.

Onani mutuwo Koperani




1 Mbiri 11:3
15 Mawu Ofanana  

Ndipo anthu Ayuda anabwera namdzoza Davide pomwepo akhale mfumu ya nyumba ya Yuda. Ndipo wina anauza Davide kuti, Anthu a ku Yabesi-Giliyadi ndiwo amene anamuika Saulo.


Chomwecho akulu onse a Israele anadza kwa mfumu ku Hebroni; ndipo mfumu Davide anapangana nao pangano ku Hebroni pamaso pa Yehova; ndipo anamdzoza Davide mfumu ya Israele.


Ku Hebroni anachita ufumu pa Yuda zaka zisanu ndi ziwiri kudza miyezi isanu ndi umodzi; ndi ku Yerusalemu anachita ufumu pa Aisraele onse ndi Ayuda omwe zaka makumi atatu mphambu zitatu.


Ndipo Yehoyada anachita chipangano pakati pa Yehova ndi mfumu ndi anthu, akhale anthu a Yehova; pakati pa mfumunso ndi anthu.


Ndipo anyamata ake anamtengera wakufa m'galeta, nabwera naye ku Yerusalemu kuchokera ku Megido, namuika m'manda akeake. Ndipo anthu a m'dziko anatenga Yehowahazi mwana wa Yosiya, namdzoza, namlonga ufumu m'malo mwa atate wake.


Akulu a amphamvu aja Davide anali nao akulimbika pamodzi naye mu ufumu wake, pamodzi ndi Aisraele onse, kumlonga ufumu, monga mwa mau a Yehova akunena za Israele, ndi awa.


Ndipo msonkhano wonse unapangana pangano ndi mfumu m'nyumba ya Mulungu. Ndipo ananena nao, Taonani, mwana wa mfumu adzakhala mfumu monga Yehova ananena za ana a Davide.


Pamenepo Yefita anamuka ndi akulu a Giliyadi, ndipo anthu anamuika mkulu wao ndi mtsogoleri wao; ndipo Yefita ananena mau ake onse pamaso pa Yehova ku Mizipa.


Ndipo anthu onse anapita ku Giligala; ndi kumeneko analonga Saulo mfumu pamaso pa Yehova mu Giligala; ndi pamenepo anaphera nsembe zoyamika pamaso pa Yehova; ndi pomwepo Saulo ndi anthu onse a Israele anakondwera kwakukulu.


Ndipo Samuele ananena naye, Yehova anang'amba ufumu wa Israele lero kuuchotsa kwa inu, naupatsa kwa mnansi wanu wina wabwino woposa inu.


Ndipo Yehova ananena ndi Samuele, Iwe ukuti ulire chifukwa cha Saulo nthawi yotani, popeza Ine ndinamkana kuti asakhale mfumu ya Israele? Dzaza nyanga yako ndi mafuta, numuke, ndidzakutumiza kwa Yese wa ku Betelehemu; pakuti ndinadzionera mfumu pakati pa ana ake.


Ndipo uitane Yese abwere kunsembeko, ndipo Ine ndidzakusonyeza chimene uyenera kuchita; ndipo udzandidzozera iye amene ndidzakutchulira dzina lake.


Ndipo awiriwo anapangana pangano pamaso pa Yehova; ndipo Davide anakhala kunkhalango, koma Yonatani anapita kunyumba yake.


Ndipo Yehova yekha wachita monga ananena pakamwa panga; ndipo Yehova wang'amba ufumuwo, kuuchotsa m'dzanja lako, ndi kuupatsa mnansi wako, ndiye Davide.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa