Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mbiri 11:2 - Buku Lopatulika

2 Ngakhale kale lomwe, pokhala mfumu Sauloyo, wotuluka ndi kulowa nao Aisraele ndinu; ndipo Yehova Mulungu wanu anati kwa inu, Uzidyetsa anthu anga Aisraele, nukhale mtsogoleri wa anthu anga Israele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ngakhale kale lomwe, pokhala mfumu Sauloyo, wotuluka ndi kulowa nao Aisraele ndinu; ndipo Yehova Mulungu wanu anati kwa inu, Uzidyetsa anthu anga Aisraele, nukhale mtsogoleri wa anthu anga Israele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Kale, ngakhale Saulo adakali mfumu yathu yotilamulira, ndinuyo amene munkatsogolera Aisraele ku nkhondo, nkumabwera nawonso. Ndipo Chauta, Mulungu wanu, adaakuuzani kuti, ‘Udzakhala mbusa wa anthu anga Aisraele, udzakhala mfumu ya anthu anga Aisraele.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Kale lija, ngakhale pamene Sauli anali mfumu, inu ndinu amene munkatsogolera Aisraeli pa nkhondo zawo. Ndipo Yehova Mulungu wanu anakuwuzani kuti, ‘Iwe udzaweta anthu anga Aisraeli, ndipo udzakhala mfumu yawo.’ ”

Onani mutuwo Koperani




1 Mbiri 11:2
16 Mawu Ofanana  

Masiku anapitawo, pamene Saulo anali mfumu yathu, inu ndinu amene munatsogolera Aisraele kutuluka nao ndi kubwera nao; ndipo Yehova ananena nanu, Uzidyetsa anthu anga Israele, ndi kukhala mtsogoleri wa Israele.


M'malo monse ndinayendamo limodzi ndi ana onse a Israele kodi ndinanena ndi fuko limodzi la Aisraele, limene ndinalamulira kudyetsa anthu anga Aisraele, kuti, Munalekeranji kundimangira nyumba yamikungudza?


Kauze Yerobowamu, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Ndingakhale ndinakukulitsa pakati pa anthu, ndi kukukhalitsa pakati pa anthu ndi kukukhalitsa mfumu ya anthu anga Aisraele,


Patsani tsono kapolo wanu mtima womvera wakuweruza anthu anu; kuti ndizindikire pakati pa zabwino ndi zoipa; pakuti akutha ndani kuweruza anthu anu ambiri amene?


Anamtenga kuja anatsata zoyamwitsa, awete Yakobo, anthu ake, ndi Israele, cholowa chake.


Iye adzadyetsa zoweta zake ngati mbusa, nadzasonkhanitsa anaankhosa m'manja mwake, nadzawatengera pa chifuwa chake, ndipo adzatsogolera bwinobwino zimene ziyamwitsa.


Taonani, ndampereka iye akhale mboni ya anthu, wotsogolera ndi wolamulira anthu.


ndipo ndidzakupatsani inu abusa monga mwa mtima wanga, adzakudyetsani inu nzeru ndi luntha.


Koma iwe, Betelehemu Efurata, ndiwe wamng'ono kuti ukhale mwa zikwi za Yuda, mwa iwe mudzanditulukira wina wakudzakhala woweruza mu Israele; matulukiro ake ndiwo a kale lomwe, kuyambira nthawi yosayamba.


Ndipo adzaimirira, nadzadyetsa nkhosa zake mu mphamvu ya Yehova, mu ukulu wa dzina la Yehova Mulungu wake; ndipo iwo adzakhalabe; pakuti pamenepo Iye adzakhala wamkulu kufikira malekezero a dziko lapansi.


wakutuluka pamaso pao, ndi kulowa pamaso pao, wakuwatulutsa ndi kuwalowetsa; kuti khamu la Yehova lisakhale ngati nkhosa zopanda mbusa.


Ndipo iwe Betelehemu, dziko la Yudeya, sukhala konse wamng'onong'ono mwa akulu a Yudeya. Pakuti Wotsogolera adzachokera mwa iwe, amene adzaweta anthu anga Aisraele.


Pamene adatulutsa zonse nkhosa zimtsata iye; chifukwa zidziwa mau ake.


Ndipo Yehova ananena ndi Samuele, Iwe ukuti ulire chifukwa cha Saulo nthawi yotani, popeza Ine ndinamkana kuti asakhale mfumu ya Israele? Dzaza nyanga yako ndi mafuta, numuke, ndidzakutumiza kwa Yese wa ku Betelehemu; pakuti ndinadzionera mfumu pakati pa ana ake.


Pamenepo Samuele anatenga nyanga ya mafuta, namdzoza pakati pa abale ake; ndipo mzimu wa Yehova unalimbika pa Davide kuyambira tsiku lomweli. Ndipo Samuele ananyamuka, nanka ku Rama.


Chifukwa chake Saulo anamchotsa kuti asakhale naye, namuika akhale mtsogoleri wake wa anthu chikwi chimodzi; ndipo iye anatsogolera anthu kutuluka ndi kubwera nao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa