Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mbiri 11:4 - Buku Lopatulika

4 Namuka Davide ndi Aisraele onse naye ku Yerusalemu, ndiwo Yebusi; ndipo Ayebusi nzika za m'dziko zinali komweko.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Namuka Davide ndi Aisraele onse naye ku Yerusalemu, ndiwo Yebusi; ndipo Ayebusi nzika za m'dziko zinali komweko.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Pambuyo pake Davide pamodzi ndi Aisraele onse adapita kukathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu, ndiye kuti Yebusi, kumene kunkakhala Ayebusi nzika za dzikolo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Davide ndi Aisraeli onse anapita ku Yerusalemu (ku Yebusi). Ayebusi amene ankakhala kumeneko

Onani mutuwo Koperani




1 Mbiri 11:4
10 Mawu Ofanana  

ndi Ayebusi, ndi Aamori, ndi Agirigasi;


ndi Aamori, ndi Akanani, ndi Agirigasi, ndi Ayebusi.


Ndipo nzika za mu Yebusi zinati kwa Davide, Sungalowe muno. Koma Davide analanda linga la Ziyoni, ndiwo mzinda wa Davide.


ndipo ndanena, Ndidzakukwezani kukutulutsani m'mazunzo a Aejipito, kukulowezani m'dziko la Akanani, ndi Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi, m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi.


Koma ana a Yuda sanakhoze kuingitsa Ayebusi, nzika za Yerusalemu: m'mwemo Ayebusi anakhala pamodzi ndi ana a Yuda, ku Yerusalemu, mpaka lero lino.


nakwera malire kunka ku chigwa cha mwana wa Hinomu, kumbali kwa Ayebusi, kumwera, ndiko Yerusalemu; nakwera malire kunka kumwamba kwa phiri lokhala patsogolo pa chigwa cha Hinomu kumadzulo, ndilo ku mathero ake a chigwa cha Refaimu kumpoto.


ndi Zela, Haelefe, ndi Yebusi, womwewo ndi Yerusalemu, Gibea ndi Kiriyati-Yearimu; mizinda khumi ndi inai pamodzi ndi midzi yake. Ndicho cholowa cha ana a Benjamini monga mwa mabanja ao.


Koma ana a Benjamini sanaingitse Ayebusi okhala mu Yerusalemu; koma Ayebusi anakhala mu Yerusalemu pamodzi ndi ana a Benjamini, mpaka lero lino.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa