Machitidwe a Atumwi 13:22 - Buku Lopatulika22 Ndipo m'mene atamchotsa iye, anawautsira Davide akhale mfumu yao; amenenso anamchitira umboni, nati, Ndapeza Davide, mwana wa Yese, munthu wa pamtima panga, amene adzachita chifuniro changa chonse. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201422 Ndipo m'mene atamchotsa iye, anawautsira Davide akhale mfumu yao; amenenso anamchitira umboni, nati, Ndapeza Davide, mwana wa Yese, munthu wa pamtima panga, amene adzachita chifuniro changa chonse. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa22 Pambuyo pake Mulungu adamchotsa Sauloyo, naika Davide kuti akhale mfumu yao. Za iyeyu Mulungu adanena kuti, ‘Ndapeza Davide, mwana wa Yese, ndiye munthu wanga wapamtima, amene adzachita zonse zimene Ine ndifuna.’ Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero22 Mulungu atamuchotsa Sauli, anayika Davide kukhala mfumu yawo. Mulungu anamuchitira umboni kuti, ‘Ndapeza Davide mwana wa Yese munthu wa pamtima panga; iye adzachita zonse zimene ine ndikufuna kuti iye achite.’ Onani mutuwo |