Pakuti Yehova ndiye wabwino; chifundo chake chimanka muyaya; ndi chikhulupiriko chake ku mibadwomibadwo.
1 Akorinto 1:9 - Buku Lopatulika Mulungu ali wokhulupirika amene munaitanidwa mwa Iye, ku chiyanjano cha Mwana wake Yesu Khristu, Ambuye wathu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mulungu ali wokhulupirika amene munaitanidwa mwa Iye, ku chiyanjano cha Mwana wake Yesu Khristu, Ambuye wathu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mulungu ndi wokhulupirika, ndipo Iye ndiye amene adakuitanani kuti mukhale a mtima umodzi ndi Mwana wake Yesu Khristu Ambuye athu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mulungu amene wakuyitanani inu mu chiyanjano ndi Mwana wake Yesu Khristu Ambuye athu ngokhulupirika. |
Pakuti Yehova ndiye wabwino; chifundo chake chimanka muyaya; ndi chikhulupiriko chake ku mibadwomibadwo.
Ndipo chilungamo chidzakhala mpango wa m'chuuno mwake, ndi chikhulupiriko chidzakhala mpango wa pa zimpso zake.
Yehova, Inu ndinu Mulungu wanga, ndidzakukuzani Inu, ndidzatamanda dzina lanu, chifukwa mwachita zinthu zodabwitsa, ngakhale zauphungu zakale, mokhulupirika ndi m'zoonadi.
Atero Yehova, Mombolo wa Israele, ndi Woyera wake, kwa Iye amene anthu amnyoza, kwa Iye amene mtundu wathu unyasidwa naye, kwa mtumiki wa olamulira: Mafumu adzaona, nadzauka; akalonga nadzalambira chifukwa cha Yehova, amene ali wokhulupirika, ngakhale Woyera wa Israele, amene anakusankha Iwe.
Mulungu sindiye munthu, kuti aname; kapena mwana wa munthu, kuti aleke; kodi anena, osachita?
kuti onse akakhale amodzi, monga Inu Atate mwa Ine, ndi Ine mwa Inu, kuti iwonso akakhale mwa Ife: kuti dziko lapansi likakhulupirire kuti Inu munandituma Ine.
Koma ngati nthambi zina zinathyoledwa, ndipo iwe, ndiwe mtengo wa azitona wakuthengo, unalumikizidwa mwa izo, nugawana nazo za muzu za mafuta ake a mtengowo,
Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake.
ndipo amene Iye anawalamuliratu, iwo anawaitananso; ndimo iwo amene Iye anawaitana, iwowa anawayesanso olungama; ndi iwo amene Iye anawayesa olungama, iwowa anawapatsanso ulemerero.
ndi ife amenenso Iye anatiitana, si a mwa Ayuda okhaokha, komanso a mwa anthu amitundu?
Koma kwa Iye muli inu mwa Khristu Yesu, amene anayesedwa kwa ife nzeru ya kwa Mulungu, ndi chilungamo ndi chiyeretso ndi chiombolo;
Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.
Chikho cha dalitso chimene tidalitsa, sichili chiyanjano cha mwazi wa Khristu kodi? Mkate umene tinyema suli chiyanjano cha thupi la Khristu kodi?
Koma pamene padakondweretsa Mulungu, amene anandipatula, ndisanabadwe, nandiitana ine mwa chisomo chake,
Ndinapachikidwa ndi Khristu; koma ndili ndi moyo; wosatinso ine ai, koma Khristu ali ndi moyo mwa ine; koma moyo umene ndili nao tsopano m'thupi, ndili nao m'chikhulupiriro cha Mwana wa Mulungu, amene anandikonda, nadzipereka yekha chifukwa cha ine.
kuti amitundu ali olowa nyumba pamodzi ndi ife, ndi ziwalo zinzathu za thupilo, ndi olandira nafe pamodzi palonjezano mwa Khristu Yesu, mwa Uthenga Wabwino,
Thanthwe, ntchito yake ndi yangwiro; pakuti njira zake zonse ndi chiweruzo; Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo; Iye ndiye wolungama ndi wolunjika.
Chifukwa chake dziwani kuti Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu; ndiye Mulungu wokhulupirika, wakusunga chipangano ndi chifundo ndi iwo akumkonda ndi kusunga malamulo ake, kufikira mibadwo zikwi.
Tsopano ndikondwera nazo zowawazo chifukwa cha inu, ndipo ndikwaniritsa zoperewera za chisautso cha Khristu m'thupi langa chifukwa cha thupi lake, ndilo Mpingowo;
ndi kukudandaulirani, ndi kukusangalatsani ndi kuchita umboni, kuti muyende koyenera Mulungu, amene akuitanani inu mulowe ufumu wake wa Iye yekha, ndi ulemerero.
kumene anaitanako inu mwa Uthenga Wabwino wathu, kuti mulandire ulemerero wa Ambuye wathu Yesu Khristu.
Koma Ambuye ali wokhulupirika amene adzakukhazikitsani inu, nadzakudikirirani kuletsa woipayo;
amene anatipulumutsa ife, natiitana ife ndi maitanidwe oyera, si monga mwa ntchito zathu, komatu monga mwa chitsimikizo mtima cha Iye yekha, ndi chisomo, chopatsika kwa ife mwa Khristu Yesu nthawi zisanayambe,
ngati tikhala osakhulupirika, Iyeyu akhala wokhulupirika; pakuti sangathe kudzikana yekha.
m'chiyembekezo cha moyo wosatha, umene Mulungu, wosanamayo, analonjeza zisanayambe nthawi zosayamba;
tigwiritse chivomerezo chosagwedera cha chiyembekezo chathu, pakuti wolonjezayo ali wokhulupirika;
Ndi chikhulupiriro Sara yemwe analandira mphamvu yakukhala ndi pakati, patapita nthawi yake, popeza anamwerengera wokhulupirika Iye amene adalonjeza;
Potero kudamuyenera kufanizidwa ndi abale m'zonse, kuti akadzakhala mkulu wa ansembe wachifundo ndi wokhulupirika m'zinthu za kwa Mulungu, kuti apereke dipo la zoipa za anthu.
Potero, abale oyera mtima, olandirana nao maitanidwe akumwamba, lingirirani za Mtumwi ndi Mkulu wa ansembe wa chivomerezo chathu, Yesu;
pakuti takhala ife olandirana ndi Khristu, ngatitu tigwiritsa chiyambi cha kutama kwathu kuchigwira kufikira chitsiriziro;
kuti mwa zinthu ziwiri zosasinthika, m'mene Mulungu sangathe kunama, tikakhale nacho chotichenjeza cholimba, ife amene tidathawira kuchigwira chiyembekezo choikika pamaso pathu;
Ndipo Mulungu wa chisomo chonse, amene adakuitanani kulowa ulemerero wake wosatha mwa Khristu, mutamva zowawa kanthawi, adzafikitsa inu opanda chilema mwini wake, adzakhazikitsa, adzalimbikitsa inu.
chimene tidachiona, ndipo tidachimva, tikulalikirani inunso, kuti inunso mukayanjane pamodzi ndi ife; ndipo chiyanjano chathu chilinso ndi Atate, ndipo ndi Mwana wake Yesu Khristu;
koma ngati tiyenda m'kuunika, monga Iye ali m'kuunika, tiyanjana wina ndi mnzake, ndipo mwazi wa Yesu Mwana wake utisambitsa kutichotsera uchimo wonse.
m'menemo tizindikira kuti tikhala mwa Iye, ndi Iye mwa ife, chifukwa anatipatsako Mzimu wake.
Ndipo ndinaona mutatseguka mu Mwamba; ndipo taonani, kavalo woyera, ndi Iye wakumkwera wotchedwa Wokhulupirika ndi Woona; ndipo aweruza, nachita nkhondo molungama.