Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 11:11 - Buku Lopatulika

11 Ndi chikhulupiriro Sara yemwe analandira mphamvu yakukhala ndi pakati, patapita nthawi yake, popeza anamwerengera wokhulupirika Iye amene adalonjeza;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndi chikhulupiriro Sara yemwe analandira mphamvu yakukhala ndi pakati, patapita nthawi yake, popeza anamwerengera wokhulupirika Iye amene adalonjeza;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Pokhala ndi chikhulupiriro, Sara yemwe adalandira mphamvu zakutenga pathupi, ngakhale zaka zake zakubala mwana zinali zitapita kale. Zimenezi zidatheka chifukwa adaavomera kuti amene adazilonjezayo ngwokhulupirika.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Ndi chikhulupiriro Sara analandira mphamvu zokhala ndi pakati ngakhale kuti zaka zake zobala mwana zinali zitapita kale, popeza anamutenga amene analonjeza kukhala wokhulupirika.

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 11:11
10 Mawu Ofanana  

Ndipo mkaziyo anaima, naona mwana wamwamuna nyengo yomweyo chaka chimene chija Elisa adanena naye.


Ndipo taona, Elizabeti mbale wako, iyenso ali ndi pakati pa mwana wamwamuna mu ukalamba wake; ndipo mwezi uno uli wachisanu ndi chimodzi wa iye amene ananenedwa wouma.


Ndiko kuti, ana a thupi sakhala iwo ana a Mulungu ai; koma ana a lonjezo awerengedwa mbeu yake.


Komatu uyo wa mdzakazi anabadwa monga mwa thupi; koma iye wa mfuluyo, anabadwa monga mwa lonjezano. Izo ndizo zophiphiritsa;


tigwiritse chivomerezo chosagwedera cha chiyembekezo chathu, pakuti wolonjezayo ali wokhulupirika;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa