1 Akorinto 10:16 - Buku Lopatulika16 Chikho cha dalitso chimene tidalitsa, sichili chiyanjano cha mwazi wa Khristu kodi? Mkate umene tinyema suli chiyanjano cha thupi la Khristu kodi? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201416 Chikho cha dalitso chimene tidalitsa, sichili chiyanjano cha mwazi wa Khristu kodi? Mkate umene tinyema suli chiyanjano cha thupi la Khristu kodi? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa16 Nanga chikho chimene timachidalitsa mothokoza Mulungu, kodi suja timaphatikizana ndi magazi a Khristu tikamweramo? Nanga mkate umene timaunyema, kodi suja timaphatikizana ndi thupi la Khristu tikaudya? Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero16 Pamene tidalitsa chikho cha Mgonero wa Ambuye, mothokoza Mulungu, kodi sitikugawana magazi a Khristu? Nanga buledi amene timanyemayo, kodi sitikugawana thupi la Khristu? Onani mutuwo |