Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa

Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano


Masalimo 29 - Buku Lopatulika Buku Lopatulika
Masalimo 29

Achenjeza akulu alemekeze Mulungu
Salimo la Davide.

1 Perekani kwa Yehova, inu ana a amphamvu, perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu.

2 Perekani kwa Yehova ulemerero wa dzina lake, gwadirani Yehova moyera ndi mokometsetsa.

3 Liu la Yehova lili pamadzi; Mulungu wa ulemerero agunda, ndiye Yehova pamadzi ambiri.

4 Liu la Yehova ndi lamphamvu; liu la Yehova ndi lalikulukulu.

5 Liu la Yehova lithyola mitengo yamkungudza; inde Yehova athyola mikungudza ya ku Lebanoni.

6 Aitumphitsa monga mwanawang'ombe; Lebanoni ndi Sirioni monga msona wa njati.

7 Liu la Yehova ligawa malawi a moto.

8 Liu la Yehova ligwedeza chipululu; Yehova agwedeza chipululu cha Kadesi.

9 Liu la Yehova liswetsa nyama zazikazi, ndipo lipulula nkhalango; ndipo mu Kachisi mwake zonse zili m'mwemo zimati, Ulemerero.

10 Yehova anakhala pa chigumula, inde Yehova akhala mfumu kunthawi yonka muyaya.

11 Yehova adzapatsa anthu ake mphamvu, Yehova adzadalitsa anthu ake ndi mtendere.

Bible Society of Malawi

Bible Society of Malawi