Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa

Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano


Masalimo 141 - Buku Lopatulika Buku Lopatulika
Masalimo 141

Davide apempha Mulungu amthandize poyesedwa ndi zoipa
Salimo la Davide.

1 Yehova, ndaitana kwa Inu; ndifulumireni ine; munditcherere khutu, pamene ndiitana kwa Inu.

2 Pemphero langa liikike ngati chofukiza pamaso panu; kukweza manja anga kuikike ngati nsembe ya madzulo.

3 Muike mdindo pakamwa panga, Yehova; sungani pakhomo pa milomo yanga.

4 Mtima wanga usalinge kuchinthu choipa, kuchita ntchito zoipa ndi anthu akuchita zopanda pake; ndipo ndisadye zankhuli zao.

5 Akandipanda munthu wolungama ndidzati nchifundo: akandidzudzula, ndidzakuyesa mafuta a pamutu; mutu wanga usakane: Pakuti pangakhale posautsidwa iwo ndidzawapempherera.

6 Oweruza ao anagwetseka pambali pa thanthwe; nadzamva mau anga kuti ndiwo okondweretsa.

7 Mafupa athu amwazika pakamwa pa manda, monga ngati akumba nanyimphula nthaka yapansi.

8 Pakuti maso anga apenya kwanu, Yehova Ambuye; ndithawira kwa Inu; musataye moyo wanga.

9 Mundisunge ndisagwe mumsampha ananditcherawo, ndisakodwe m'makwekwe a iwo ochita zopanda pake.

10 Oipa agwe pamodzi m'maukonde ao, kufikira nditapitirira ine.

Bible Society of Malawi

Bible Society of Malawi