Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa

Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano


Masalimo 112 - Buku Lopatulika Buku Lopatulika
Masalimo 112

Adalitsidwa akuopa Mulungu

1 Aleluya. Wodala munthu wakuopa Yehova, wakukondwera kwambiri ndi malamulo ake.

2 Mbeu yake idzakhala yamphamvu padziko lapansi; mbadwo wa oongoka mtima udzadalitsidwa.

3 M'nyumba mwake mudzakhala akatundu ndi chuma: Ndi chilungamo chake chikhala chikhalire.

4 Kuunika kutulukira oongoka mtima mumdima; Iye ndiye wachisomo, ndi wansoni ndi wolungama.

5 Wodala munthu wakuchitira chifundo, nakongoletsa; adzalimbika nao mlandu wake poweruzidwa.

6 Popeza sadzagwedezeka nthawi zonse; wolungama adzakumbukika ku nthawi yosatha.

7 Sadzaopa mbiri yoipa; mtima wake ngwokhazikika, wokhulupirira Yehova.

8 Mtima wake ngwochirikizika, sadzachita mantha, kufikira ataona chofuna iye pa iwo omsautsa.

9 Anagawagawa, anapatsa aumphawi; chilungamo chake chikhalitsa kosatha; nyanga yake idzakwezeka ndi ulemu.

10 Woipa adzaziona, nadzapsa mtima; adzakukuta mano, nadzasungunuka; chokhumba oipa chidzatayika.

Bible Society of Malawi

Bible Society of Malawi