Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


45 Mau a Mulungu Pa Mayesero

45 Mau a Mulungu Pa Mayesero

Ndipotu, cholinga cha Mulungu chachikulu ndikuti tisinthe tsiku ndi tsiku kukhala ngati Mwana wake Yesu. Choncho, cholinga chathu chachikulu monga Akhristu chiyenera kukhala kuphunzira ndi kusintha kuti tizitsatira mtima wa Mulungu. Zonse zomwe zimachitika m'moyo, ngakhale mavuto ndi mayesero, zimathandiza kuti tikwaniritse cholinga chimenechi.

Monga mmene lemba la 1 Petro 1:6-7 limatiuza, "M’menemo mumakondwera, ngakhale tsopano, ngati kuli kofunikira, mukuvutika ndi mayesero osiyanasiyana, kuti chikhulupiriro chanu, chimene chiposa golidi wosawonongeka, choyesedwa ndi moto, chikapezeke choyenera kuyamika, ulemerero ndi ulemu pa kubwera kwa Yesu Khristu." Mayesero amene timakumana nawo amalimbitsa chikhulupiriro chathu, ndi kutithandiza kudalira Mulungu podziwa kuti Iye ndi weniweni komanso wokhulupirika nthawi zonse.




Yakobo 1:2-3

Muchiyese chimwemwe chokha, abale anga, m'mene mukugwa m'mayesero a mitundumitundu; Pakuti mkwiyo wa munthu suchita chilungamo cha Mulungu. Mwa ichi, mutavula chinyanso chonse ndi chisefukiro cha choipa, landirani ndi chifatso mau ookedwa mwa inu, okhoza kupulumutsa moyo wanu. Khalani akuchita mau, osati akumva okha, ndi kudzinyenga nokha. Pakuti ngati munthu ali wakumva mau, wosati wakuchita, iyeyu afanana ndi munthu wakuyang'anira nkhope yake ya chibadwidwe chake m'kalirole; pakuti wadziyang'anira yekha, nachoka, naiwala pompaja nali wotani. Koma iye wakupenyerera m'lamulo langwiro, ndilo laufulu, natero chipenyerere, ameneyo, posakhala wakumva wakuiwala, komatu wakuchita ntchito, adzakhala wodala m'kuchita kwake. Ngati wina adziyesera ali wopembedza Mulungu, ndiye wosamanga lilime lake, koma adzinyenga mtima wake, kupembedza kwake kwa munthuyu nkopanda pake. Mapembedzedwe oyera ndi osadetsa pamaso pa Mulungu ndi Atate ndiwo: kucheza ndi ana amasiye ndi akazi amasiye m'chisautso chao, ndi kudzisungira mwini wosachitidwa mawanga ndi dziko lapansi. pozindikira kuti chiyesedwe cha chikhulupiriro chanu chichita chipiriro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:2-4

Muchiyese chimwemwe chokha, abale anga, m'mene mukugwa m'mayesero a mitundumitundu; Pakuti mkwiyo wa munthu suchita chilungamo cha Mulungu. Mwa ichi, mutavula chinyanso chonse ndi chisefukiro cha choipa, landirani ndi chifatso mau ookedwa mwa inu, okhoza kupulumutsa moyo wanu. Khalani akuchita mau, osati akumva okha, ndi kudzinyenga nokha. Pakuti ngati munthu ali wakumva mau, wosati wakuchita, iyeyu afanana ndi munthu wakuyang'anira nkhope yake ya chibadwidwe chake m'kalirole; pakuti wadziyang'anira yekha, nachoka, naiwala pompaja nali wotani. Koma iye wakupenyerera m'lamulo langwiro, ndilo laufulu, natero chipenyerere, ameneyo, posakhala wakumva wakuiwala, komatu wakuchita ntchito, adzakhala wodala m'kuchita kwake. Ngati wina adziyesera ali wopembedza Mulungu, ndiye wosamanga lilime lake, koma adzinyenga mtima wake, kupembedza kwake kwa munthuyu nkopanda pake. Mapembedzedwe oyera ndi osadetsa pamaso pa Mulungu ndi Atate ndiwo: kucheza ndi ana amasiye ndi akazi amasiye m'chisautso chao, ndi kudzisungira mwini wosachitidwa mawanga ndi dziko lapansi. pozindikira kuti chiyesedwe cha chikhulupiriro chanu chichita chipiriro. Koma chipiriro chikhale nayo ntchito yake yangwiro, kuti mukakhale angwiro ndi opanda chilema, osasowa kanthu konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:12

Wodala munthu wakupirira poyesedwa; pakuti pamene wavomerezeka, adzalandira korona wa moyo, amene Ambuye adalonjezera iwo akumkonda Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:7

kuti mayesedwe a chikhulupiriro chanu, ndiwo a mtengo wake woposa wa golide amene angotayika, ngakhale ayesedwa ndi moto, akapezedwe ochitira chiyamiko ndi ulemerero ndi ulemu pa vumbulutso la Yesu Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 23:10

Koma adziwa njira ndilowayi; atandiyesa ndidzatuluka ngati golide.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:3-5

Ndipo si chotero chokha, komanso tikondwera m'zisautso; podziwa ife kuti chisautso chichita chipiriro; ndi chipiriro chichita chizolowezi; ndi chizolowezi chichita chiyembekezo: ndipo chiyembekezo sichichititsa manyazi; chifukwa chikondi cha Mulungu chinatsanulidwa m'mitima mwathu mwa Mzimu Woyera, amene wapatsidwa kwa ife.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:6

M'menemo mukondwera, kungakhale tsopano kanthawi, ngati kuyenera, mukachitidwe chisoni ndi mayesero a mitundumitundu,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 17:3

Mwayesera mtima wanga; mwandizonda usiku; mwandisuntha, simupeza kanthu; mwatsimikiza mtima kuti m'kamwa mwanga simudzalakwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:4

ndi chizolowezi chichita chiyembekezo:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 1:3

kwa iwonso anadzionetsera yekha wamoyo ndi zitsimikizo zambiri, zitatha zowawa zake, naonekera kwa iwo masiku makumi anai, ndi kunena zinthu za Ufumu wa Mulungu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 2:9

Pakuti chifukwa cha ichi ndalembanso, kuti ndidziwe mayesedwe anu, ngati muli omvera m'zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 2:4

komatu monga Mulungu anativomereza kutiikiza Uthenga Wabwino, kotero tilankhula; osati monga okondweretsa anthu, koma Mulungu; amene ayesa mitima yathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 41:13

Pakuti Ine Yehova Mulungu wako ndidzagwira dzanja lako lamanja, ndi kunena kwa iwe, Usaope ndidzakuthandiza iwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:13

Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:6-7

M'menemo mukondwera, kungakhale tsopano kanthawi, ngati kuyenera, mukachitidwe chisoni ndi mayesero a mitundumitundu, kuti mayesedwe a chikhulupiriro chanu, ndiwo a mtengo wake woposa wa golide amene angotayika, ngakhale ayesedwa ndi moto, akapezedwe ochitira chiyamiko ndi ulemerero ndi ulemu pa vumbulutso la Yesu Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:23

Mundisanthule, Mulungu, nimudziwe mtima wanga; mundiyese nimudziwe zolingalira zanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 26:2

Mundiyesere, Yehova, ndipo mundisunthe; yeretsani impso zanga ndi mtima wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:7

ndi kutaya pa Iye nkhawa yanu yonse, pakuti Iye asamalira inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:3-4

Ndipo si chotero chokha, komanso tikondwera m'zisautso; podziwa ife kuti chisautso chichita chipiriro; ndi chipiriro chichita chizolowezi; ndi chizolowezi chichita chiyembekezo:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 8:16

amene anakudyetsani m'chipululu ndi mana, amene makolo anu sanawadziwe; kuti akuchepetseni, ndi kuti akuyeseni, kuti akuchitireni chokoma potsiriza panu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 66:10-12

Pakuti munatiyesera, Mulungu, munatiyenga monga ayenga siliva. Munapita nafe kuukonde; munatisenza chothodwetsa pamsana pathu. Munapititsa anthu oberekeka pamwamba pamitu pathu; tinapyola moto ndi madzi; koma munatifikitsa potitsitsimutsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:4

Koma yense ayesere ntchito yake ya iye yekha, ndipo pamenepo adzakhala nako kudzitamandira chifukwa cha iye yekha, si chifukwa cha wina.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:1-2

Chifukwa chake ifenso, popeza tizingidwa nao mtambo waukulu wotere wa mboni, titaye cholemetsa chilichonse, ndi tchimoli limangotizinga, ndipo tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira, ndi kupenyerera woyambira ndi womaliza wa chikhulupiriro chathu, Pakutitu iwo anatilanga masiku owerengeka monga kudawakomera; koma Iye atero, kukatipindulitsa, kuti tikalandirane nao pa chiyero chake. Chilango chilichonse, pakuchitika, sichimveka chokondweretsa, komatu chowawa; koma chitatha, chipereka chipatso cha mtendere, kwa iwo ozoloweretsedwa nacho, ndicho cha chilungamo. Mwa ichi limbitsani manja ogooka, ndi maondo olobodoka; ndipo lambulani miseu yolunjika yoyendamo mapazi anu, kuti chotsimphinacho chisapatulidwe m'njira, koma chichiritsidwe. Londolani mtendere ndi anthu onse, ndi chiyeretso chimene, akapanda ichi, palibe mmodzi adzaona Ambuye: ndi kuyang'anira kuti pangakhale wina wakuperewera chisomo cha Mulungu, kuti ungapuke muzu wina wa kuwawa mtima ungavute inu, ndipo aunyinji angadetsedwe nao; kuti pangakhale wachigololo, kapena wamnyozo, ngati Esau, amene anagulitsa ukulu wake wobadwa nao mtanda umodzi wa chakudya. Pakuti mudziwa kutinso pamene anafuna kulowa dalitsolo, anakanidwa (pakuti sanapeze malo akulapa), angakhale analifunafuna ndi misozi. Pakuti simunayandikire phiri lokhudzika, ndi lakupsa moto, ndi pakuda bii, ndi mdima, ndi namondwe, ndi mau a lipenga, ndi manenedwe a mau, manenedwe amene iwo adamvawo anapempha kuti asawaonjezerepo mau; Yesu, ameneyo, chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira mtanda, nanyoza manyazi, nakhala padzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 27:1

Yehova ndiye kuunika kwanga ndi chipulumutso changa; ndidzaopa yani? Yehova ndiye mphamvu ya moyo wanga; ndidzachita mantha ndi yani?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:17-18

ndipo ngati ana, pomweponso olowa nyumba; inde olowa nyumba ake a Mulungu, ndi olowa anzake a Khristu; ngatitu ife timva zowawa pamodzi naye, kuti tikalandirenso ulemerero pamodzi ndi Iye. Pakuti ndiyesa kuti masauko a nyengo yatsopano sayenera kulinganizidwa ndi ulemerero umene udzaonetsedwa kwa ife.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 10:13

Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:28

Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:5-6

Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; umlemekeze m'njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:9

Koma tisaleme pakuchita zabwino; pakuti pa nyengo yake tidzatuta tikapanda kufooka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:71

Kundikomera kuti ndinazunzidwa; kuti ndiphunzire malemba anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 17:3

Siliva ali ndi mbiya yosungunulira, golide ali ndi ng'anjo; koma Yehova ayesa mitima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 1:21-22

nati, Ndinatuluka m'mimba ya mai wanga wamaliseche, wamaliseche ndidzamukanso; Yehova anapatsa, Yehova watenga, lidalitsike dzina la Yehova. Mwa ichi chonse Yobu sanachimwe, kapena kunenera Mulungu cholakwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 2:12

ngati tipirira, tidzachitanso ufumu ndi Iye: ngati timkana Iye, Iyeyunso adzatikana ife:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 14:22

nalimbikitsa mitima ya ophunzira, nadandaulira iwo kuti akhalebe m'chikhulupiriro, ndi kuti tiyenera kulowa mu ufumu wa Mulungu ndi zisautso zambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 94:19

Pondichulukira zolingalira zanga m'kati mwanga, zotonthoza zanu zikondweretsa moyo wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 4:12-13

Okondedwa, musazizwe ndi mayesedwe amoto adakugwerani inu akhale chakukuyesani, ngati chinthu chachilendo chachitika nanu: koma popeza mulawana ndi Khristu zowawa zake, kondwerani: kutinso pa vumbulutso la ulemerero wake mukakondwere kwakukulukulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:13

Mwa ichi mudzitengere zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoza kuima chitsutsire pofika tsiku loipa, ndipo, mutachita zonse, mudzachilimika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:12

kondwerani m'chiyembekezo, pirirani m'masautso; limbikani chilimbikire m'kupemphera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:10-12

Odala ali akuzunzidwa chifukwa cha chilungamo: chifukwa uli wao Ufumu wa Kumwamba. Odala muli inu m'mene adzanyazitsa inu, nadzazunza inu, nadzakunenerani monama zoipa zilizonse chifukwa cha Ine. Sekerani, sangalalani: chifukwa mphotho yanu ndi yaikulu mu Mwamba: pakuti potero anazunza aneneri anakhalawo musanabadwe inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 3:12

Ndipo onse akufuna kukhala opembedza m'moyo mwa Khristu Yesu, adzamva mazunzo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 118:5-6

M'mene ndinasautsika ndinaitanira pa Yehova; anandiyankha nandiika motakasuka Yehova. Yehova ndi wanga; sindidzaopa; adzandichitanji munthu?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:19

Masautso a wolungama mtima achuluka, koma Yehova amlanditsa mwa onsewa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 3:3-4

kuti asasunthike wina ndi zisautso izi, pakuti mudziwa nokha kuti adatiika ife tichite izi. Pakutinso, pamene tinali ndi inu tinakuuziranitu kuti tidzamva zisautso; monga kudachitika, monganso mudziwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 43:2

Pamene udulitsa pamadzi ndili pamodzi ndi iwe; ndi pooloka mitsinje sidzakukokolola; pakupyola pamoto sudzapsa; ngakhale lawi silidzakutentha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Wanga, Mpulumutsi! Lero ndikufuulirani, ndikufuna nkhope yanu kuti ndikupatseni ulemerero ndi ulemu. Ndikukupemphani mundipatse mphamvu nthawi yovuta ino yomera ndikuyesedwa. Ambuye, ndithandizeni kupita patsogolo, kuti ndizipitirizabe kuyenda ngakhale madzi akundikana. Ndadziwa kuti ndinu ngalawa yanga, ndinu chikhulupiriro changa, ndipo mumatsitsimula mphepo yamkuntho m'moyo mwanga. Zikomo, Ambuye, chifukwa ndimatha kupereka nkhawa zanga zonse kwa inu, podziwa kuti mudzandisamalira ndi kundipatsa mtendere pakati pa mayesero. Mumawu anu mukuti: “Iwo okonda Mulungu, zinthu zonse zigwirira pamodzi kuwachitira iwo zabwino, iwowa okhala otchedwa monga mwa chifuniro chake.” Pasadakhale ndikukuthankirani chifukwa cha chipambano, chifukwa ndikulengeza kuti sindidzatuluka m'nthawi yoyesedwa ino momfanana, koma idzabala mwa ine ulemerero wosatha, chifukwa ndikudziwa kuti mukupanga mwa ine chikhulupiriro ndi khalidwe la wokhulupirira woona. M'dzina la Yesu. Ameni!
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa