Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Miyambo 17:3 - Buku Lopatulika

3 Siliva ali ndi mbiya yosungunulira, golide ali ndi ng'anjo; koma Yehova ayesa mitima.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Siliva ali ndi mbiya yosungunulira, golide ali ndi ng'anjo; koma Yehova ayesa mitima.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Siliva amamuyesera m'chitofu, golide amamuyesera m'ng'anjo, koma mitima amaiyesa ndi Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Siliva amamuyesa mʼngʼanjo ndipo golide amamuyesa mʼngʼanjo, koma Yehova amayesa mitima.

Onani mutuwo Koperani




Miyambo 17:3
21 Mawu Ofanana  

Ndidziwanso, Mulungu wanga, kuti muyesa mtima, nimukondwera nako kuongoka. Koma ine, ndi mtima wanga woongoka ndapereka zonsezi mwaufulu; ndipo tsopano ndaona mokondwera anthu anu okhala pompano, napereka kwa Inu mwaufulu.


Koma adziwa njira ndilowayi; atandiyesa ndidzatuluka ngati golide.


Koma kuli mtapo wa siliva, ndi malo a golide amene amuyenga.


Mundisanthule, Mulungu, nimudziwe mtima wanga; mundiyese nimudziwe zolingalira zanga.


Mundiyesere, Yehova, ndipo mundisunthe; yeretsani impso zanga ndi mtima wanga.


Pakuti munatiyesera, Mulungu, munatiyenga monga ayenga siliva.


Kumanda ndi kuchionongeko kuli pamaso pa Yehova; koposa kotani nanga mitima ya ana a anthu?


Njira zonse za munthu ziyera pamaso pake; koma Yehova ayesa mizimu.


Kapolo wochita mwanzeru adzalamulira mwana wochititsa manyazi, nadzagawana nao abale cholowa.


Njira zonse za munthu zilungama pamaso pake; koma Yehova ayesa mitima.


Siliva asungunuka m'mbiya, ndi golide m'ng'anjo, motero chomwe munthu achitama adziwika nacho.


Taona ndakuyenga, koma si monga siliva, ndakuyesa iwe m'ng'anjo ya masautso.


Ine Yehova ndisanthula mtima, ndiyesa impso, kuti ndimpatse munthu yense monga mwa njira zake, monga zipatso za ntchito zake.


Wobadwa ndi munthu iwe, nyumba ya Israele yandikhalira mphala; onsewo ndiwo mkuwa, ndi seta, ndi chitsulo, ndi ntovu, m'kati mwa ng'anjo; ndiwo mphala zasiliva.


Nadzagwa aphunzitsi ena kuwayesa ndi moto, ndi kuwatsutsa, ndi kuwayeretsa, mpaka nthawi ya chitsiriziro; pakuti kukaliko kufikira nthawi yoikika.


Ndi gawo lachitatulo ndidzalitengera kumoto, ndi kuwayenga ngati ayenga siliva, ndi kuwayesa monga ayesa golide; adzaitana dzina langa, ndipo ndidzawamvera; ndidzati, Awa ndi anthu anga; ndi iwo adzati, Yehova ndi Mulungu wanga.


amene anakudyetsani m'chipululu ndi mana, amene makolo anu sanawadziwe; kuti akuchepetseni, ndi kuti akuyeseni, kuti akuchitireni chokoma potsiriza panu;


Ndipo mukumbukire njira yonse imene Yehova Mulungu wanu anakuyendetsani m'chipululu zaka izi makumi anai, kuti akuchepetseni, kukuyesani, kudziwa chokhala mumtima mwanu, ngati mudzasunga malamulo ake, kapena iai.


kuti mayesedwe a chikhulupiriro chanu, ndiwo a mtengo wake woposa wa golide amene angotayika, ngakhale ayesedwa ndi moto, akapezedwe ochitira chiyamiko ndi ulemerero ndi ulemu pa vumbulutso la Yesu Khristu;


Ndipo ndidzaononga ana ake ndi imfa; ndipo idzazindikira Mipingo yonse kuti Ine ndine Iye amene ayesa impso ndi mitima; ndipo ndidzaninkha kwa yense wa inu monga mwa ntchito zanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa