Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Timoteyo 3:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo onse akufuna kukhala opembedza m'moyo mwa Khristu Yesu, adzamva mazunzo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo onse akufuna kukhala opembedza m'moyo mwa Khristu Yesu, adzamva mazunzo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Onse ofuna kukhala ndi moyo wolemekeza Mulungu mwa Khristu Yesu, adzazunzikadi,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Kunena zoona, munthu aliyense amene akufuna kukhala moyo wolemekeza Mulungu mwa Khristu Yesu, adzazunzikadi,

Onani mutuwo Koperani




2 Timoteyo 3:12
32 Mawu Ofanana  

Pomwepo Yesu anati kwa ophunzira ake, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, natenge mtanda wake, nanditsate Ine.


Chifukwa cha icho, onani, ndituma kwa inu aneneri ndi anzeru ndi alembi; ena a iwo mudzawapha, mudzawapachika; ndi ena a iwo mudzawakwapula m'masunagoge mwanu, ndi kuwazunza, kuchokera kumudzi umodzi, kufikira kumudzi wina;


amene sadzalandira makumi khumi tsopano nthawi ino, nyumba, ndi abale, ndi alongo, ndi amai, ndi ana, ndi minda, pamodzi ndi mazunzo; ndipo nthawi ilinkudza, moyo wosatha.


Adzakutulutsani m'masunagoge, koma ikudza nthawi imene yense wakupha inu adzayesa kuti atumikira Mulungu.


Zinthu izi ndalankhula ndi inu, kuti mwa Ine mukakhale nao mtendere. M'dziko lapansi mudzakhala nacho chivuto, koma limbikani mtima; ndalingonjetsa dziko lapansi Ine.


Ine ndawapatsa iwo mau anu; ndipo dziko lapansi, linadana nao, chifukwa sakhala a dziko lapansi, monga Ine sindikhala wa dziko lapansi.


nalimbikitsa mitima ya ophunzira, nadandaulira iwo kuti akhalebe m'chikhulupiriro, ndi kuti tiyenera kulowa mu ufumu wa Mulungu ndi zisautso zambiri.


Ngati tiyembekezera Khristu m'moyo uno wokha, tili ife aumphawi oposa a anthu onse.


Pakuti kudzitamandira kwathu ndiko umboni wa chikumbumtima chathu, kuti m'chiyero ndi kuona mtima kwa Mulungu, si m'nzeru ya thupi, koma m'chisomo cha Mulungu tinadzisunga m'dziko lapansi, koma koposa kwa inu.


olondoleka, koma osatayika; ogwetsedwa, koma osaonongeka;


chifukwa cha mafumu ndi onse akuchita ulamuliro; kuti m'moyo mwathu tikakhale odika mtima ndi achete m'kulemekeza Mulungu, ndi m'kulemekezeka monse.


Ndipo povomerezeka, chinsinsi cha kuchitira Mulungu ulemu nchachikulu: Iye amene anaonekera m'thupi, anayesedwa wolungama mumzimu, anapenyeka ndi angelo, analalikidwa mwa amitundu, wokhulupiridwa m'dziko lapansi, wolandiridwa mu ulemerero.


Ngati munthu aphunzitsa zina, wosavomerezana nao mau a moyowo a Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi chiphunzitsocho chili monga mwa chipembedzo:


Paulo, kapolo wa Mulungu, ndi mtumwi wa Yesu Khristu, monga mwa chikhulupiriro cha osankhika a Mulungu, ndi chizindikiritso cha choonadi chili monga mwa chipembedzo,


ndi kutiphunzitsa ife kuti, pokana chisapembedzo ndi zilakolako za dziko lapansi, tikhale ndi moyo m'dziko lino odziletsa, ndi olungama, ndi opembedza;


Pamenepo ana a Yosefe ananena ndi Yoswa, ndi kuti, Watipatsiranji cholowa chathu chamaere chimodzi ndi gawo limodzi, popeza ife ndife anthu aunyinji, pakuti Yehova anatidalitsa ndi pano pomwe?


Komatu ngatinso mukumva zowawa chifukwa cha chilungamo, odala inu; ndipo musaope pakuwaopa iwo, kapena musadere nkhawa;


Popeza izi zonse zidzakanganuka kotero, muyenera inu kukhala anthu otani nanga, m'mayendedwe opatulika ndi m'chipembedzo,


Ndipo mchira wake uguza limodzi la magawo atatu a nyenyezi zam'mwamba, nuziponya padziko. Ndipo chinjoka chinaimirira pamaso pa mkazi akuti abale, kuti, akabala icho chikalikwire mwana wake.


Ndipo ndinati kwa iye, Mbuye wanga, mudziwa ndinu. Ndipo anati kwa ine, Iwo ndiwo akutuluka m'chisautso chachikulu; ndipo anatsuka zovala zao, naziyeretsa m'mwazi wa Mwanawankhosa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa