Ndipo Yehova anautsira Yehoramu mzimu wa Afilisti, ndi wa Aarabu okhala pambali pa Akusi;
Yoweli 3:4 - Buku Lopatulika Ndiponso ndili ndi chiyani ndi inu, Tiro ndi Sidoni, ndi malire onse a Filistiya? Mudzandibwezera chilango kodi? Mukandibwezera chilango msanga, mofulumira, ndidzabwezera chilango chanu pamutu panu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndiponso ndili ndi chiyani ndi inu, Tiro ndi Sidoni, ndi malire onse a Afilisti? Mudzandibwezera chilango kodi? Mukandibwezera chilango msanga, mofulumira, ndidzabwezera chilango chanu pamutu panu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Kodi inu a ku Tiro, a ku Sidoni ndi a ku madera a Filistiya, mukuti mundichite chiyani? Kodi mumati mundilipsirire chifukwa cha zina zimene ine ndakuchitani? Ngati pali kanthu koti mundilipsirire, ndidzabwezera zochita zanu zonse pamutu panu mofulumira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Kodi tsopano inu a ku Turo ndi Sidoni ndi madera onse a Filisitiya, muli ndi chiyani chotsutsana nane? Kodi mukundibwezera pa zinthu zimene ndakuchitirani? Ngati inu mukundibwezera, Ine ndidzabwezera zochita zanu mofulumira ndi mwachangu pa mitu yanu. |
Ndipo Yehova anautsira Yehoramu mzimu wa Afilisti, ndi wa Aarabu okhala pambali pa Akusi;
Usakondwere, iwe Filistiya, wonsewe, pothyoka ndodo inakumenya; pakuti m'muzu wa njoka mudzatuluka mphiri, ndimo chipatso chake chidzakhala njoka yamoto youluka.
Pakuti lili tsiku la kubwezera la Yehova, chaka chakubwezera chilango, mlandu wa Ziyoni.
Monga mwa ntchito zao momwemo Iye adzabwezera amaliwongo ake ukali, nadzabwezera adani ake chilango; nadzabwezeranso zisumbu chilango.
Mau a Yehova amene anadza kwa Yeremiya mneneri onena za Afilisti, Farao asanakanthe Gaza.
chifukwa cha tsiku lakudzafunkha Afilisti onse, kuphera Tiro ndi Sidoni othangata onse akutsala; pakuti Yehova adzafunkha Afilisti, otsala a chisumbu cha Kafitori.
Thawani pakati pa Babiloni, yense apulumuke moyo wake; musathedwe m'choipa chake; pakuti ndi nthawi ya kubwezera chilango; Yehova adzambwezera iye mphotho yake.
Dziko lapansi linjenjemera pamaso pao, thambo ligwedezeka, dzuwa ndi mwezi zada, ndi nyenyezi zibweza kuwala kwao;
tsiku la mdima, la mdima wandiweyani, tsiku la mitambo, mitambo yochindikira, ngati m'mbandakucha moyalika pamapiri; mtundu waukulu ndi wamphamvu, panalibe wotere ndi kale lonse, sipadzakhalanso wotere utapita uwu, kufikira zaka za mibadwo yambiri.
Tsoka kwa iwe, Korazini! Tsoka kwa iwe, Betsaida! Chifukwa ngati zamphamvu zimene zachitidwa mwa inu zikadachitidwa mu Tiro ndi mu Sidoni, akadatembenuka mtima kalekale m'ziguduli ndi m'phulusa.
Komanso ndinena kwa inu kuti tsiku la kuweruza mlandu wao wa Tiro ndi Sidoni udzachepa ndi wanu.
Tsoka iwe, Korazini! Tsoka iwe Betsaida! Chifukwa kuti zikadachitika mu Tiro ndi Sidoni zamphamvuzi zidachitika mwa inu, akadalapa kale lomwe ndi kukhala pansi ovala chiguduli ndi phulusa.
Ndipo kodi Mulungu sadzachitira chilungamo osankhidwa ake akumuitana usana ndi usiku, popeza aleza nao mtima?
Kubwezera chilango nkwanga, kubwezera komwe, pa nyengo ya kuterereka phazi lao; pakuti tsiku la tsoka lao layandika, ndi zinthu zowakonzeratu zifulumira kudza.
Ndipo Yefita anatuma mithenga kwa mfumu ya ana a Amoni, ndi kuti, Ndi chiyani ndi inu ndi kuti mwandidzera kuthira nkhondo dziko langa?