Luka 10:13 - Buku Lopatulika13 Tsoka iwe, Korazini! Tsoka iwe Betsaida! Chifukwa kuti zikadachitika mu Tiro ndi Sidoni zamphamvuzi zidachitika mwa inu, akadalapa kale lomwe ndi kukhala pansi ovala chiguduli ndi phulusa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201413 Tsoka iwe, Korazini! Tsoka iwe Betsaida! Chifukwa kuti zikadachitika m'Tiro ndi Sidoni zamphamvuzi zidachitika mwa inu, akadalapa kale lomwe ndi kukhala pansi ovala chiguduli ndi phulusa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa13 “Uli ndi tsoka, iwe Korazini! Uli ndi tsoka, iwe Betsaida! Chifukwa zamphamvu zimene zidachitika mwa inu, achikhala zidaachitikira ku Tiro ndi ku Sidoni, bwenzi anthu ake atavala kale ziguduli nkudzithira phulusa, kuwonetsa kuti atembenukadi mtima. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero13 “Ndiwe watsoka, iwe Korazini! Ndiwe watsoka, iwe Betisaida! Kukanakhala kuti zodabwitsa zimene zinachitika mwa inu zinachitika ku Turo ndi Sidoni, iwo akanatembenuka mtima kale lomwe, atavala ziguduli ndi kudzola phulusa. Onani mutuwo |