Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 11:21 - Buku Lopatulika

21 Tsoka kwa iwe, Korazini! Tsoka kwa iwe, Betsaida! Chifukwa ngati zamphamvu zimene zachitidwa mwa inu zikadachitidwa mu Tiro ndi mu Sidoni, akadatembenuka mtima kalekale m'ziguduli ndi m'phulusa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Tsoka kwa iwe, Korazini! Tsoka kwa iwe, Betsaida! Chifukwa ngati zamphamvu zimene zachitidwa mwa inu zikadachitidwa m'Tiro ndi m'Sidoni, akadatembenuka mtima kalekale m'ziguduli ndi m'phulusa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Adati, “Uli ndi tsoka iwe Korazini! Uli ndi tsoka iwe Betsaida! Chifukwa zamphamvu zimene zidachitika mwa inu, achikhala zidaachitikira ku Tiro ndi ku Sidoni, bwenzi anthu ake atavala kale ziguduli nkudzithira phulusa, kuwonetsa kuti atembenukadi mtima.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 “Tsoka kwa iwe Korazini! Tsoka kwa iwe Betisaida! Ngati zodabwitsa zimene zinachitika mwa iwe zikanachitidwa mu Turo ndi Sidoni, iwo akanalapa kale atavala ziguduli ndi kudzola phulusa.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 11:21
31 Mawu Ofanana  

chifukwa chake ndekha ndidzinyansa, ndi kulapa m'fumbi ndi mapulusa.


Ndaona zonyansa zako, ndi zigololo zako, ndi zakumemesa zako, ndi chinyerinyeri cha dama lako, pamapiri ndi m'munda. Tsoka kwa iwe, Yerusalemu! Sudzayeretsedwa; kodi zidzatero mpaka liti?


Ndiponso ndili ndi chiyani ndi inu, Tiro ndi Sidoni, ndi malire onse a Filistiya? Mudzandibwezera chilango kodi? Mukandibwezera chilango msanga, mofulumira, ndidzabwezera chilango chanu pamutu panu.


Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Tiro, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anapereka anthu onse kwa Edomu, osakumbukira pangano lachibale;


Komanso ndinena kwa inu kuti tsiku la kuweruza mlandu wao wa Tiro ndi Sidoni udzachepa ndi wanu.


Ndipo Yesu anatulukapo napatukira kumbali za Tiro ndi Sidoni.


Tsoka lili ndi dziko lapansi chifukwa cha zokhumudwitsa! Pakuti sikutheka kuti zokhumudwitsa zileke kudza, koma tsoka lili ndi munthu amene chokhumudwitsacho chidza ndi iye.


Mwana wa Munthu achokatu, monga kunalembedwa za Iye; koma tsoka ali nalo munthu amene Mwana wa Munthu aperekedwa ndi iye! Kukadakhala bwino kwa munthuyo ngati sakadabadwa.


ndi a ku Yerusalemu, ndi a ku Idumeya, ndi a ku tsidya lina la Yordani, ndi a kufupi ku Tiro ndi Sidoni, khamu lalikulu, pakumva zazikuluzo anazichita, linadza kwa Iye.


Ndipo pomwepo Iye anakakamiza ophunzira ake alowe m'ngalawa, ndi kumtsogolera kutsidya lija ku Betsaida, m'mene Iye yekha alimkuuza khamulo kuti amuke.


Ndipo Iye anauka nachoka kumeneko, nanka ku maiko a ku Tiro ndi Sidoni. Ndipo analowa m'nyumba, nafuna kuti asadziwe anthu; ndipo sanakhoze kubisika.


Ndipo anatulukanso m'maiko a ku Tiro, nadzera pakati pa Sidoni, kufikira ku nyanja ya Galileya, ndi kupyola pakati pa maiko a ku Dekapoli.


Ndipo anadza ku Betsaida. Ndipo anadza naye kwa Iye munthu wakhungu, nampempha Iye kuti amkhudze.


ndipo Eliya sanatumidwe kwa mmodzi wa iwo, koma ku Sarepta wa ku Sidoni, kwa mkazi wamasiye.


Ndipo Iye anatsika nao, naima pachidikha, ndi khamu lalikulu la ophunzira ake, ndi unyinji waukulu wa anthu a ku Yudeya yense ndi Yerusalemu, ndi a ku mbali ya nyanja ya ku Tiro ndi Sidoni, amene anadza kudzamva Iye ndi kudzachiritsidwa nthenda zao;


Ndipo atabwera atumwi, anamfotokozera Iye zonse anazichita. Ndipo Iye anawatenga, napatuka nao pa okha kunka kumzinda dzina lake Betsaida.


Koma Filipo anali wa ku Betsaida, mzinda wa Andrea ndi Petro.


Ndipo iwo anadza kwa Filipo wa ku Betsaida wa mu Galileya, namfunsa iye, ndi kuti, Mbuye, tifuna kuona Yesu.


Koma Herode anaipidwa nao a ku Tiro ndi Sidoni; ndipo anamdzera iye ndi mtima umodzi, ndipo m'mene adakopa Blasito mdindo wa mfumu, anapempha mtendere, popeza dziko lao linapeza zakudya zochokera ku dziko la mfumu.


Ndipo m'mawa mwake tinangokocheza ku Sidoni; ndipo Julio anachitira Paulo mwachikondi, namlola apite kwa abwenzi ake amchereze.


Tsoka kwa iwo! Pakuti anayenda m'njira ya Kaini, ndipo anadziononga m'chisokero cha Balamu chifukwa cha kulipira, natayika m'chitsutsano cha Kora.


Ndipo ndidzalamulira mboni zanga ziwiri, ndipo zidzanenera masiku chikwi chimodzi ndi mazana awiri amphambu makumi asanu ndi limodzi, zovala chiguduli.


Ndipo ndinaona pamene anamasula chizindikiro chachisanu ndi chimodzi, ndipo panali chivomezi chachikulu; ndi dzuwa lidada bii longa chiguduli cha ubweya ndi mwezi wonse unakhala ngati mwazi;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa