Inu mudzauka, ndi kuchitira nsoni Ziyoni; popeza yafika nyengo yakumchitira chifundo, nyengo yoikika.
Yohane 7:6 - Buku Lopatulika Chifukwa chake Yesu ananena nao, Nthawi yanga siinafike; koma nthawi yanu yakonzeka masiku onse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa chake Yesu ananena nao, Nthawi yanga siinafike; koma nthawi yanu yakonzeka masiku onse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adaŵauza kuti, “Nthaŵi yanga siinafikebe, koma yanu ndi nthaŵi iliyonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho Yesu anawawuza iwo kuti, “Nthawi yanga yoyenera sinafike; kwa inu nthawi ina iliyonse ndi yoyenera. |
Inu mudzauka, ndi kuchitira nsoni Ziyoni; popeza yafika nyengo yakumchitira chifundo, nyengo yoikika.
Nati Iye, Mukani kumzinda kwa munthu wina wake, mukati kwa Iye, Mphunzitsi anena, Nthawi yanga yayandikira; ndidzadya Paska kwanu pamodzi ndi ophunzira anga.
Koma pasanafike chikondwerero la Paska, Yesu, podziwa kuti nthawi yake idadza yakuchoka kutuluka m'dziko lino lapansi, kunka kwa Atate, m'mene anakonda ake a Iye yekha a m'dziko lapansi, anawakonda kufikira chimaliziro.
Zinthu izi analankhula Yesu; ndipo m'mene anakweza maso ake Kumwamba, anati, Atate, yafika nthawi; lemekezani Mwana wanu, kuti Mwana wanu akulemekezeni Inu;
Pamenepo anafuna kumgwira Iye; koma palibe wina anamgwira kumanja, chifukwa nthawi yake siinafike.
Kwerani inu kunka kuphwando; sindikwera Ine kuphwando ili tsopano apa; pakuti nthawi yanga siinakwanire.
Mau awa analankhula m'nyumba yosungiramo chuma cha Mulungu pophunzitsa mu Kachisi; ndipo palibe munthu anamgwira Iye, pakuti nthawi yake siinafike.
Koma anati kwa iwo, Sikuli kwa inu kudziwa nthawi kapena nyengo, zimene Atate anaziika mu ulamuliro wake wa Iye yekha.