Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 8:20 - Buku Lopatulika

20 Mau awa analankhula m'nyumba yosungiramo chuma cha Mulungu pophunzitsa mu Kachisi; ndipo palibe munthu anamgwira Iye, pakuti nthawi yake siinafike.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Mau awa analankhula m'nyumba yosungiramo chuma cha Mulungu pophunzitsa m'Kachisi; ndipo palibe munthu anamgwira Iye, pakuti nthawi yake siinafike.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Yesu adanena mau ameneŵa pamene ankaphunzitsa m'Nyumba ya Mulungu, m'chipinda cholandiriramo zopereka za anthu. Panalibe amene adamgwira, chifukwa nthaŵi yake inali isanafike.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Iye anayankhula mawu awa pamene amaphunzitsa Nyumba ya Mulungu pafupi ndi malo amene amaponyapo zopereka. Komabe palibe amene anamugwira Iye, chifukwa nthawi yake inali isanakwane.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 8:20
17 Mawu Ofanana  

pakuti odikira anai aakulu, ndiwo Alevi, anali mu udindo wao, nayang'anira zipinda ndi mosungiramo chuma m'nyumba ya Mulungu.


Nthawi yomweyo Yesu anati kwa makamuwo a anthu, Kodi munatulukira kundigwira Ine ndi malupanga ndi mikunkhu, ngati wachifwamba? Tsiku ndi tsiku ndimakhala mu Kachisi kuphunzitsa, ndipo simunandigwire.


Ndipo ansembe aakulu anatenga ndalamazo, nati, Sikuloledwa kuziika m'chosonkhera ndalama za Mulungu, chifukwa ndizo mtengo wa mwazi.


Ndipo Iye anakhala pansi pandunji pa mosungiramo ndalama, napenya kuti khamu la anthu alikuponya ndalama mosungiramo; ndipo eni chuma ambiri anaponyamo zambiri.


Ndipo anaitana ophunzira ake, nati kwa iwo, Ndithu ndinena ndi inu, Mkazi wamasiye amene waumphawi anaponya zambiri koposa onse akuponya mosungiramo:


Ndipo alembi ndi ansembe aakulu anafunafuna kumgwira ndi manja nthawi yomweyo; ndipo anaopa anthu; pakuti anazindikira kuti ananenera pa iwo fanizo ili.


Ndipo Yesu anakweza maso, naona anthu eni chuma alikuika zopereka zao mosungiramo ndalama.


Anafunanso kumgwira Iye; ndipo anapulumuka m'dzanja lao.


Yesu nanena naye, Mkazi, ndili ndi chiyani ndi inu? Nthawi yanga siinafike.


Koma pamene padafika pakati pa chikondwerero, Yesu anakwera nalowa mu Kachisi, naphunzitsa.


Pamenepo anafuna kumgwira Iye; koma palibe wina anamgwira kumanja, chifukwa nthawi yake siinafike.


Koma ena mwa iwo anafuna kumgwira Iye; koma palibe munthu anamgwira kumanja.


Kwerani inu kunka kuphwando; sindikwera Ine kuphwando ili tsopano apa; pakuti nthawi yanga siinakwanire.


Koma mamawa anadzanso ku Kachisi, ndipo anthu onse anadza kwa Iye; ndipo m'mene anakhala pansi anawaphunzitsa.


Pamenepo anatola miyala kuti amponye Iye; koma Yesu anabisala, natuluka mu Kachisi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa