Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 8:21 - Buku Lopatulika

21 Pamenepo anatinso kwa iwo; Ndimuka Ine, ndipo mudzandifuna, ndipo m'tchimo lanu mudzafa: kumene ndimukako Ine, simudziwa kudza inu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Pamenepo anatinso kwa iwo; Ndimuka Ine, ndipo mudzandifuna, ndipo m'tchimo lanu mudzafa: kumene ndimukako Ine, simudziwa kudza inu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Pambuyo pake Yesu adaŵauzanso kuti, “Ine ndikupita. Mudzandifunafuna koma mudzafera m'machimo anu. Kumene ndikupita Ine, inu simungathe kufikako.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Kenakanso Yesu anawawuza kuti, “Ine ndikupita, ndipo mudzandifunafuna, koma mudzafa muli mʼmachimo anu. Kumene ndikupita, inu simungabwereko.”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 8:21
21 Mawu Ofanana  

Pali Yehova Mulungu wanu, ngati kuli mtundu umodzi wa anthu, kapena ufumu, kumene mbuye wanga sananditumeko kukufunani, ndipo pakunena iwo, Palibe iye, analumbiritsa ufumu umene ndi mtundu umene kuti sanakupezeni.


Mafupa ake adzala nao unyamata wake, koma udzagona naye pansi m'fumbi.


Pomwalira woipa chidikiro chake chionongeka; chiyembekezo cha uchimo chionongeka.


Wochimwa adzakankhidwa m'kuipa kwake; koma wolungama akhulupirirabe pomwalira.


Sipadzakhalanso khanda la masiku, pena munthu wokalamba osakwanitsa masiku ake; pakuti mwana adzafa wa zaka zana limodzi; ndipo wochimwa pokhala wa zaka zana limodzi adzatemberedwa.


Pakuti ndinena kwa inu, Simudzandionanso Ine, kuyambira tsopano, kufikira mudzanena, Wolemekezedwa Iye amene akudza m'dzina la Ambuye.


Pomwepo Iye adzanena kwa iwo a kudzanja lamanzere, Chokani kwa Ine otembereredwa inu, kumoto wa nthawi zonse wokolezedwera mdierekezi ndi angelo ake:


Ndipo amenewa adzachoka kunka ku chilango cha nthawi zonse; koma olungama kumoyo wa nthawi zonse.


Koma ananena ichi ndi kuzindikiritsa imfa yanji akuti adzafa nayo.


Pamenepo Yesu anati kwa iwo, Katsala kanthawi kakang'ono ndipo kuunika kuli mwa inu. Yendani pokhala muli nako kuunika, kuti mdima sungakupezeni; ndipo woyenda mumdima sadziwa kumene amukako.


Tiana, katsala kanthawi ndikhala ndi inu. Mudzandifunafuna Ine; ndipo monga ndinanena kwa Ayuda, kuti kumene ndinkako Ine, inu simungathe kudza, momwemo ndinena kwa inu tsopano.


Mudzafunafuna Ine, osandipeza; ndipo pomwe ndili Ine, inu simungathe kudzapo.


Mau awa amene ananena ndi chiyani, Mudzandifunafuna osandipeza Ine: ndipo pomwe ndili Ine, inu simungathe kudzapo?


Chifukwa chake ndinati kwa inu, kuti mudzafa m'machimo kwa inu, kuti mudzafa m'machimo anu, pakuti ngati simukhulupirira kuti Ine ndine, mudzafa m'machimo anu.


Ndipo inu, anakupatsani moyo, pokhala munali akufa ndi zolakwa, ndi zochimwa zanu,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa