Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 17:1 - Buku Lopatulika

1 Zinthu izi analankhula Yesu; ndipo m'mene anakweza maso ake Kumwamba, anati, Atate, yafika nthawi; lemekezani Mwana wanu, kuti Mwana wanu akulemekezeni Inu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Zinthu izi analankhula Yesu; ndipo m'mene anakweza maso ake Kumwamba, anati, Atate, yafika nthawi; lemekezani Mwana wanu, kuti Mwana wanu akulemekezeni Inu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Yesu atanena zimenezi, adayang'ana kumwamba nati, “Atate, yafika nthaŵi. Lemekezani Mwana wanu, kuti Mwanayo akulemekezeni Inu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Yesu atatha kunena izi, anayangʼana kumwamba ndipo anapemphera: “Atate, nthawi yafika. Lemekezani Mwana wanu, kuti Mwana wanuyo akulemekezeni Inu.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 17:1
20 Mawu Ofanana  

Ndikweza maso anga kwa Inu, kwa Inu wakukhala kumwamba.


Ndinalankhulalankhula ngati namzeze, pena chumba; Ndinalira maliro ngati nkhunda; maso anga analephera pogadamira kumwamba. Ambuye ndasautsidwa, mundiperekere chikoli.


Ndipo anadza kachitatu, nanena nao, Gonani tsopano, nimupumule; chakwanira; yafika nthawi; onani Mwana wa Munthu aperekedwa m'manja a anthu ochimwa.


Koma wamsonkhoyo alikuima patali sanafune kungakhale kukweza maso kumwamba, komatu anadziguguda pachifuwa pake nanena, Mulungu, mundichitire chifundo, ine wochimwa.


Masiku onse, pamene ndinali ndi inu mu Kachisi, simunatanse manja anu kundigwira: koma nyengo ino ndi yanu, ndipo ulamuliro wa mdima ndi wanu.


Koma Yesu pamene anamva, anati, Kudwala kumene sikuli kwa imfa, koma chifukwa cha ulemerero wa Mulungu, kuti Mwana wa Mulungu alemekezedwe nako.


Pomwepo anachotsa mwala. Koma Yesu anakweza maso ake kupenya kumwamba nati, Atate, ndiyamika Inu kuti munamva Ine.


Koma Yesu anayankha iwo, nati, Yafika nthawi, kuti Mwana wa Munthu alemekezedwe.


Koma pasanafike chikondwerero la Paska, Yesu, podziwa kuti nthawi yake idadza yakuchoka kutuluka m'dziko lino lapansi, kunka kwa Atate, m'mene anakonda ake a Iye yekha a m'dziko lapansi, anawakonda kufikira chimaliziro.


Onani ikudza nthawi, ndipo yafika, imene mudzabalalitsidwa, yense ku zake za yekha, ndipo mudzandisiya Ine pa ndekha. Ndipo sindikhala pa ndekha, chifukwa Atate ali pamodzi ndi Ine,


Pamenepo anafuna kumgwira Iye; koma palibe wina anamgwira kumanja, chifukwa nthawi yake siinafike.


Koma ichi anati za Mzimu, amene iwo akukhulupirira Iye anati adzalandire; pakuti Mzimu panalibe pamenepo, chifukwa Yesu sanalemekezedwe panthawi pomwepo.


Mau awa analankhula m'nyumba yosungiramo chuma cha Mulungu pophunzitsa mu Kachisi; ndipo palibe munthu anamgwira Iye, pakuti nthawi yake siinafike.


Mulungu wa Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo, Mulungu wa makolo athu, analemekeza Mwana wake Yesu; amene inu munampereka ndi kumkaniza pa Pilato, poweruza iyeyu kummasula.


chifukwa cha inu amene mwa Iye mukhulupirira Mulungu wakumuukitsa Iye kwa akufa, ndi kumpatsa Iye ulemerero; kotero kuti chikhulupiriro chanu ndi chiyembekezo chanu chikhale pa Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa