Ndipo inayalidwa ndi mkungudza pamwamba pa zipinda makumi anai mphambu zisanu zolongosoledwa pa mapanda, mzere umodzi zipinda khumi mphambu asanu.
Numeri 5:3 - Buku Lopatulika muwatulutse amuna ndi akazi muwatulutsire kunja kwa chigono, kuti angadetse chigono chao, chimene ndikhala m'kati mwakemo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 muwatulutse amuna ndi akazi muwatulutsire kunja kwa chigono, kuti angadetse chigono chao, chimene ndikhala m'kati mwakemo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Muchotse anthu onse otere, amuna kapena akazi. Muziŵatulutsira kunja kwa zithando kuti angaipitse zithando zao, poti Ine ndimakhala pakati pa anthu anga.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Muchotse amuna komanso amayi ndipo muwatulutsire kunja kwa msasa kuti asadetse msasa wawo kumene Ine ndimakhala pakati pawo.” |
Ndipo inayalidwa ndi mkungudza pamwamba pa zipinda makumi anai mphambu zisanu zolongosoledwa pa mapanda, mzere umodzi zipinda khumi mphambu asanu.
Munakwera kunka kumwamba, munapita nao undende kuuyesa ndende; munalandira zaufulu mwa anthu, ngakhale mwa opikisana nanu, kuti Yehova Mulungu akakhale nao.
Tafuula, takuwa iwe, wokhala mu Ziyoni, chifukwa Woyera wa Israele wa m'kati mwako ali wamkulu.
Ndipo iye wakuti ayeretsedwe atsuke zovala zake, namete tsitsi lake lonse, nasambe madzi, nakhale woyera; ndipo atatero alowe kuchigono, koma agone pa bwalo la hema wake masiku asanu ndi awiri.
Motero muzipatula ana a Israele kwa kudetsedwa kwao; angafe m'kudetsedwa kwao, pamene adetsa chihema changa ali pakati pao.
Ndipo anasonkhana motsutsana pa Mose ndi Aroni, nanena nao, Mukula mphamvu inu, pakuti khamu lonse nlopatulika, onsewa, ndipo Yehova ali pakati pao; mudzikuza bwanji pa msonkhano wa Yehova?
Ndipo chilichonse munthu wodetsedwa achikhudza chidzakhala chodetsedwa; ndi munthu wakuchikhudza adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
Usamadetsa dziko ukhala m'mwemo, limene ndikhalitsa pakati pake; popeza Ine Yehova ndikhalitsa pakati pa ana a Israele.
Ndipo ana a Israele anachita chotero, nawatulutsira kunja kwa chigono; monga Yehova adanena ndi Mose momwemo ana a Israele anachita.
popeza Yehova Mulungu wanu ayenda pakati pa chigono chanu kukupulumutsani ndi kupereka adani anu pamaso panu; chifukwa chake chigono chanu chikhale chopatulika; kuti angaone kanthu kodetsa mwa inu, ndi kukupotolokerani.
Ndipo tikulamulirani, abale, m'dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti mubwevuke kwa mbale yense wakuyenda dwakedwake, wosatsata mwambo umene anaulandira kwa ife.
ndipo simudzalowa konse momwemo kanthu kalikonse kosapatulidwa kapena iye wakuchita chonyansa ndi bodza; koma iwo okha olembedwa m'buku la moyo la Mwanawankhosa.
Ndipo ndinamva mau aakulu ochokera ku mpando wachifumu, ndi kunena Taonani, chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nao, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nao, Mulungu wao;