Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 35:34 - Buku Lopatulika

34 Usamadetsa dziko ukhala m'mwemo, limene ndikhalitsa pakati pake; popeza Ine Yehova ndikhalitsa pakati pa ana a Israele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

34 Usamadetsa dziko ukhala m'mwemo, limene ndikhalitsa pakati pake; popeza Ine Yehova ndikhalitsa pakati pa ana a Israele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

34 Musaipitse dziko limene mukukhalamo, dziko limene Inenso ndikukhalamo. Paja Ine Chauta ndimakhala pakati pa Aisraele.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

34 Choncho musadetse dziko limene mukukhalamo, dziko limene Inenso ndimakhalamo, pakuti Ine Yehova, ndimakhala pakati pa Aisraeli.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Numeri 35:34
20 Mawu Ofanana  

Ndipo ndidzakhala pakati pa ana a Israele osawasiya anthu anga a Israele.


Pampumulo panga mpano posatha, Pano ndidzakhala; pakuti ndakhumbapo.


Alemekezedwe Yehova kuchokera mu Ziyoni, amene akhala mu Yerusalemu. Aleluya.


Ndipo andimangire malo opatulika; kuti ndikhale pakati pao.


Pakuti atero Iye amene ali wamtali wotukulidwa, amene akhala mwachikhalire, amene dzina lake ndiye Woyera, Ndikhala m'malo aatali ndi oyera, pamodzi ndi yense amene ali wa mzimu wosweka ndi wodzichepetsa, kutsitsimutsa mzimu wa odzichepetsa, ndi kutsitsimutsa mtima wa osweka.


Musachinene, Chiwembu; chilichonse chimene anthu awa adzachinena, Chiwembu; musaope monga kuopa kwao kapena musachite mantha.


Poyamba ndibwezera mphulupulu yao ndi tchimo lao chowirikiza; chifukwa anaipitsa dziko langa ndi mitembo ya zodetsedwa zao, nadzaza cholowa changa ndi zonyansa zao.


Popeza wanena, Mitundu iwiri iyi ya anthu ndi maiko awiri awa adzakhala anga, tidzakhala nao ngati cholowa chathu, angakhale Yehova anali komweko;


Sadzakhala m'dziko la Yehova; koma Efuremu adzabwerera kunka ku Ejipito; ndipo adzadya chakudya chodetsa mu Asiriya.


Ndipo anasonkhana motsutsana pa Mose ndi Aroni, nanena nao, Mukula mphamvu inu, pakuti khamu lonse nlopatulika, onsewa, ndipo Yehova ali pakati pao; mudzikuza bwanji pa msonkhano wa Yehova?


muwatulutse amuna ndi akazi muwatulutsire kunja kwa chigono, kuti angadetse chigono chao, chimene ndikhala m'kati mwakemo.


mtembo wake usakhale pamtengo usiku wonse, koma mumuike ndithu tsiku lomwelo; pakuti wopachikidwa pamtengo atembereredwa ndi Mulungu; kuti mungadetse dziko lanu limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale cholowa chanu.


Landirani, Yehova, chotetezera anthu anu Israele, amene munawaombola, ndipo musalole mwazi wosachimwa ukhale pakati pa anthu anu Israele; ndipo adzawatetezera cha mwaziwo.


pakuti Yehova Mulungu wanu ali pakati panu, ndiye Mulungu wansanje; kuti ungapse mtima wa Yehova Mulungu wanu, ndi kukuonongani, kukuchotsani pankhope padziko lapansi.


ndipo simudzalowa konse momwemo kanthu kalikonse kosapatulidwa kapena iye wakuchita chonyansa ndi bodza; koma iwo okha olembedwa m'buku la moyo la Mwanawankhosa.


Ndipo ndinamva mau aakulu ochokera ku mpando wachifumu, ndi kunena Taonani, chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nao, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nao, Mulungu wao;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa