Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 5:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Muchotse amuna komanso amayi ndipo muwatulutsire kunja kwa msasa kuti asadetse msasa wawo kumene Ine ndimakhala pakati pawo.”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

3 muwatulutse amuna ndi akazi muwatulutsire kunja kwa chigono, kuti angadetse chigono chao, chimene ndikhala m'kati mwakemo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 muwatulutse amuna ndi akazi muwatulutsire kunja kwa chigono, kuti angadetse chigono chao, chimene ndikhala m'kati mwakemo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Muchotse anthu onse otere, amuna kapena akazi. Muziŵatulutsira kunja kwa zithando kuti angaipitse zithando zao, poti Ine ndimakhala pakati pa anthu anga.”

Onani mutuwo Koperani




Numeri 5:3
23 Mawu Ofanana  

Pamwamba pa mitandapo panali matabwa a mkungudza amene anaphimba zipinda zimene zinamangidwa pa nsanamira 45, pa mzere uliwonse nsanamira 15.


Pamene Inu munakwera mmwamba, munatsogolera a mʼndende ambiri; munalandira mphatso kuchokera kwa anthu, ngakhale kuchokera kwa owukira, kuti Inu Mulungu, mukhale kumeneko.


“Iwo andipangire malo wopatulika, ndipo Ine ndidzakhala pakati pawo.


Ndidzakhala pakati pa Aisraeli ndikukhala Mulungu wawo.


Fuwulani ndi kuyimba mwachimwemwe, inu anthu a ku Ziyoni; pakuti Woyerayo wa Israeli ndi wamkulu pakati panu.”


“Munthu amene wayeretsedwa uja achape zovala zake, amete tsitsi lake lonse, ndipo asambe mʼmadzi. Akatero adzakhala woyeretsedwa. Atatha zimenezi munthuyo apite ku msasa wake koma akhale kunja kwa msasawo kwa masiku asanu ndi awiri.


“ ‘Choncho muwayeretsa ana a Israeli nʼkudetsedwa kwawo kuti angafe pochita tchimo lowadetsa limene polichita limadetsa malo anga wokhalamo amene ali pakati pawo.’ ”


Iwo anasonkhana kudzatsutsana ndi Mose ndi Aaroni nawawuza kuti, “Mwawonjeza! Anthu onsewa ndi oyera, aliyense wa iwo, ndipo Yehova ali pakati pawo. Chifukwa chiyani mukudzikuza pakati pa gulu lonse la Yehova?”


Chilichonse chimene munthu wodetsedwayo achikhudze chidzakhala chodetsedwa ndiponso aliyense wochikhudza adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.”


Choncho musadetse dziko limene mukukhalamo, dziko limene Inenso ndimakhalamo, pakuti Ine Yehova, ndimakhala pakati pa Aisraeli.’ ”


Aisraeli anachitadi zimenezi. Anawatulutsira kunja kwa msasa monga momwe Yehova analamulira Mose.


Pakuti Yehova Mulungu wanu amayendayenda ku msasa wanu kukutchinjirizani ndi kupereka adani anu kwa inu. Nʼchifukwa chake msasa wanu uzikhala wopatulika kuti mwina angaone china chonyansa nabwerera osakuyandikirani.


Ngati kapolo wathawa mbuye wake nakabisala kwanu, musamuperekenso kwa mbuye wakeyo.


Abale, tikukulamulani mʼdzina la Ambuye Yesu Khristu, kuti mupewe mʼbale aliyense amene ndi waulesi ndi wachisokonezo, wosafuna kutsata zimene tinakuphunzitsani.


Munthu woyambitsa mipatuko umuchenjeze koyamba, ndiponso umuchenjeze kachiwiri. Kenaka umupewe.


Kanthu kosayeretsedwa sikadzalowamo, kuphatikizanso aliyense wochita zinthu zochititsa manyazi ndi zachinyengo, koma okhawo amene mayina awo alembedwa mʼbuku lamoyo la Mwana Wankhosa.


Ndipo ndinamva mawu ofuwula kuchokera ku Mpando Waufumu kuti, “Taonani! Malo wokhalapo Mulungu ali pakati pa anthu, ndipo Iye adzakhala ndi anthuwo. Iwo adzakhala anthu ake ndipo Mulungu mwini adzakhala nawo nakhala Mulungu wawo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa