Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 5:2 - Buku Lopatulika

2 Uza ana a Israele kuti azitulutsa m'chigono akhate onse, ndi onse akukhala nako kukha, ndi onse odetsedwa chifukwa cha akufa;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Uza ana a Israele kuti azitulutsa m'chigono akhate onse, ndi onse akukhala nako kukha, ndi odetsedwa chifukwa cha akufa;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 “Lamula Aisraele kuti achotse wakhate aliyense m'zithando, aliyense wotulutsa zinthu zoipa m'thupi mwake, ndiponso munthu wodziipitsa pokhudza mtembo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 “Lamula Aisraeli kuti achotse mu msasa aliyense amene ali ndi matenda opatsirana a pa khungu kapena matenda otuluka madzi mʼthupi a mtundu uliwonse, kapena aliyense wodetsedwa chifukwa cha munthu wakufa.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 5:2
15 Mawu Ofanana  

Koma polowera pa chipata panali amuna anai akhate, nanenana wina ndi mnzake, Tikhaliranji kuno mpaka kufa?


Ndipo azing'amba zovala zake za wakhate ali ndi nthendayo, ndi tsitsi la pamutu pake lizikhala lomasuka, naphimbe iye mlomo wake wa m'mwamba, nafuule, Wodetsedwa, wodetsedwa!


Masiku onse nthenda ikali pa iye azikhala wodetsedwa; ali wodetsedwa, agone pa yekha pokhala pake pakhale kunja kwa chigono.


ndipo wansembe aone, ndipo taonani, ngati nkhanambo yapitirira khungu, wansembe amutche wodetsedwa, ndilo khate.


Ndipo iye wakuti ayeretsedwe atsuke zovala zake, namete tsitsi lake lonse, nasambe madzi, nakhale woyera; ndipo atatero alowe kuchigono, koma agone pa bwalo la hema wake masiku asanu ndi awiri.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Nena ndi ansembe, ana a Aroniwo, nuti nao, Asadzidetse mmodzi wa inu chifukwa cha wakufa mwa anthu a mtundu wake;


Pakuti munthu aliyense wosadzichepetsa tsiku limenelo, amsadze kwa anthu a mtundu wake.


Ndipo mtambo unachoka pachihema; ndipo taonani, Miriyamu anali wakhate, wa mbuu ngati chipale chofewa; ndipo Aroni anapenya Miriyamu, taonani, anali wakhate.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Atate wake akadamlavulira malovu pankhope pake sakadachita manyazi masiku asanu ndi awiri? Ambindikiritse kunja kwa chigono masiku asanu ndi awiri; ndipo atatero amlandirenso.


Ndipo mukhale m'misasa kunja kwa chigono masiku asanu ndi awiri; aliyense adapha munthu, ndi aliyense wakukhudza wophedwa, mudziyeretse tsiku lachitatu ndi lachisanu ndi chiwiri, inu ndi andende anu.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa