Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Numeri 34:11 - Buku Lopatulika

ndi malire adzatsika ku Sefamu kunka ku Ribula, kum'mawa kwa Aini; ndipo malire adzatsika, nadzafikira mbali ya nyanja ya Kinereti kum'mawa,

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

ndi malire adzatsika ku Sefamu kunka ku Ribula, kum'mawa kwa Aini; ndipo malire adzatsika, nadzafikira mbali ya nyanja ya Kinereti kum'mawa,

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Atsike kuchokera ku Sefamu mpaka ku Ribula, kuvuma kwa Aini. Atsikebe mpaka ku gombe la Nyanja ya Galilea, kuvuma,

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Malirewo adzatsikire ku Sefamu mpaka ku Ribila cha kummawa kwa Aini ndi kupitirira mpaka ku matsitso a cha kummawa kwa Nyanja ya Kinereti.

Onani mutuwo



Numeri 34:11
16 Mawu Ofanana  

Ndipo Farao Neko anammanga mu Ribula, m'dziko la Hamati; kuti asachite ufumu mu Yerusalemu; nasonkhetsa dzikoli msonkho wa matalente zana limodzi la siliva, ndi talente limodzi la golide.


Ndipo anaigwira mfumu, nakwera nayo kwa mfumu ya Babiloni ku Ribula, naweruza mlandu wake.


Ndipo mfumu ya ku Babiloni inapha ana a Zedekiya pamaso pake; niphanso akulu onse a Yuda mu Ribula.


Ndipo anamgwira iye, namtengera kwa mfumu ya ku Babiloni ku Ribula m'dziko la Hamati; ndipo iye anamweruza.


Ndipo mudzilembere malire a kum'mawa ochokera ku Hazara-Enani kunka ku Sefamu;


ndi malire adzatsika ku Yordani, ndi kutuluka kwake kudzakhala ku Nyanja ya Mchere; ili ndili dziko lanu monga mwa malire ake polizinga.


Ndipo pamene iwo anaoloka, anafika kumtunda, ku Genesarete.


Ndipo panali, pakumkanikiza khamu la anthu, kudzamva mau a Mulungu, Iye analikuimirira m'mbali mwa nyanja ya Genesarete;


Zitapita izi anachoka Yesu kunka kutsidya lija la nyanja ya Galileya, ndiyo ya Tiberiasi.


ndi chidikha, ndi Yordani ndi malire ake, kuyambira ku Kinereti kufikira ku Nyanja ya Araba, ndiyo Nyanja ya Mchere, patsinde pa Pisiga, kum'mawa.


ndi kwa mafumu akukhala kumpoto kumapiri, ndi kuchigwa kumwera kwa Kineroti, ndi kuchidikha, ndi ku mitunda ya Dori kumadzulo;


ndi pachidikha mpaka nyanja ya Kineroti kum'mawa, ndi mpaka nyanja ya kuchidikha, ndiyo Nyanja ya Mchere kum'mawa, njira ya Beteyesimoti; ndi kumwera pansi pa matsikiro a Pisiga.


ndipo m'chigwa Beteharamu, ndi Betenimura, ndi Sukoti, ndi Zafoni, chotsala cha ufumu wa Sihoni mfumu ya Hesiboni, Yordani ndi malire ake, mpaka malekezero a nyanja ya Kinereti, tsidya lija la Yordani kum'mawa.


Ndipo mizinda yamalinga ndiyo Zidimu, Zeri, ndi Hamati, Rakati, ndi Kinereti;