Yeremiya 52:9 - Buku Lopatulika9 Ndipo anamgwira iye, namtengera kwa mfumu ya ku Babiloni ku Ribula m'dziko la Hamati; ndipo iye anamweruza. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Ndipo anamgwira iye, namtengera kwa mfumu ya ku Babiloni ku Ribula m'dziko la Hamati; ndipo iye anamweruza. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 Apo a ku Babiloni aja atamgwira Zedekiya, adapita naye kwa Nebukadinezara, ku Ribula m'dziko la Hamati. Komweko Nebukadinezarayo adagamula mlandu wa Zedekiya uja. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Anagwidwa napita naye kwa mfumu ya ku Babuloni ku Ribula mʼdziko la Hamati, kumene anagamula mlandu wake. Onani mutuwo |
Ndipo pambuyo pake, ati Yehova, ndidzapereka Zedekiya mfumu ya Yuda, ndi atumiki ake, ndi anthu, ngakhale a m'mzinda uwu amene asiyidwa ndi mliri, ndi lupanga, ndi njala, m'dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, ndi m'dzanja la adani ao, ndi m'dzanja la amene afuna moyo wao; ndipo adzawakantha ndi lupanga lakuthwa; osawaleka, osachita chisoni, osachita chifundo.