Taonani, nditi ndilimangire dzina la Yehova Mulungu wanga nyumba, kumpatulira iyo, ndi kufukiza pamaso pake zonunkhira za fungo lokoma, ndiyo ya mkate woonekera wachikhalire, ndi ya nsembe zopsereza, m'mawa ndi madzulo, pamasabata, ndi pokhala mwezi, ndi pa zikondwerero zoikika za Yehova Mulungu wathu. Ndiwo machitidwe osatha mu Israele.
monga momwe mudayenera, tsiku ndi tsiku; napereka monga momwe adauza Mose pamasabata, pokhala mwezi, ndi pa zikondwerero zoikika, katatu m'chaka: pa chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa, ndi pa chikondwerero cha Masabata, ndi pa chikondwerero cha Misasa.
Ndipo tsiku la Sabata anaankhosa awiri a chaka chimodzi, opanda chilema, ndi awiri a magawo khumi a efa wa ufa wosalala, ukhale nsembe yaufa, wosakaniza ndi mafuta, ndi nsembe yake yothira;
tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo, pamodzi ndi nsembe yauchimo yotetezera, ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira.
pamodzi ndi nsembe yopsereza ya pamwezi, ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira, monga mwa lemba lake, zikhale za fungo lokoma, nsembe yamoto ya Yehova.